Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 15:1-33

15  Kuyankha modekha kumabweza mkwiyo,+ koma mawu opweteka amayambitsa mkwiyo.+  Lilime la anthu anzeru limalankhula zabwino zimene anthuwo akudziwa,+ koma pakamwa pa zitsiru pamasefukira mawu opusa.+  Maso a Yehova ali paliponse.+ Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.+  Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo,+ koma lilime lachinyengo limapweteketsa mtima.+  Aliyense wopusa amanyoza malangizo* a bambo ake,+ koma munthu aliyense womvera chidzudzulo ndi wochenjera.+  M’nyumba ya munthu wolungama muli katundu wambiri,+ koma katundu wa munthu woipa amabweretsa tsoka.+  Milomo ya anzeru imafalitsa zimene ikudziwa,+ koma mtima wa anthu opusa suchita zimenezo.+  Nsembe ya anthu oipa imam’nyansa Yehova,+ koma pemphero la anthu owongoka mtima limam’sangalatsa.+  Yehova amanyansidwa ndi njira ya munthu woipa,+ koma iye amakonda munthu wochita chilungamo.+ 10  Munthu wosiya njira yabwino amadana ndi malangizo.+ Aliyense wodana ndi chidzudzulo adzafa.+ 11  Manda ndiponso malo a chiwonongeko+ zili pamaso pa Yehova.+ Ndiye kuli bwanji mitima ya ana a anthu?+ 12  Munthu wonyoza amadana ndi munthu amene akum’dzudzula.+ Iye sadzapita kwa anthu anzeru.+ 13  Mtima wachimwemwe umapangitsa nkhope kusangalala,+ koma chifukwa cha kupweteka kwa mtima munthu sasangalala.+ 14  Mtima womvetsa ndi umene umafunafuna kudziwa zinthu,+ koma pakamwa pa anthu opusa m’pamene pamafunafuna kulankhula zopusa.+ 15  Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa,+ koma munthu wamtima wosangalala amachita phwando nthawi zonse.+ 16  Ndi bwino kukhala ndi zinthu zochepa ukuopa Yehova,+ kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri koma uli ndi nkhawa.+ 17  Ndi bwino kudya zamasamba koma pali chikondi,+ kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali chidani.+ 18  Munthu wopsa mtima amayambitsa mkangano,+ koma munthu wosakwiya msanga amaziziritsa mkangano.+ 19  Njira ya munthu waulesi ili ngati mpanda wa mitengo yaminga,+ koma njira ya anthu owongoka mtima imakhala yosalazidwa bwino.+ 20  Mwana wanzeru ndi amene amakondweretsa bambo ake,+ koma wopusa amanyoza mayi ake.+ 21  Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amakondwera ndi uchitsiru,+ koma munthu wozindikira ndi amene amayenda panjira yabwino.+ 22  Zolingalira sizikwaniritsidwa ngati anthu sakambirana moona mtima,+ koma aphungu akachuluka zimakwaniritsidwa.+ 23  Munthu amasangalala ndi yankho lochokera pakamwa pake,+ ndipo mawu onenedwa pa nthawi yoyenera ndi abwino kwambiri.+ 24  Njira ya kumoyo ndi yowongoka kwa munthu wochita zanzeru,+ kuti asatsikire pansi ku Manda.+ 25  Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+ 26  Ziwembu za munthu woipa ndi zonyansa kwa Yehova,+ koma mawu osangalatsa ndi oyera pamaso pake.+ 27  Munthu wopeza phindu mwachinyengo amabweretsa tsoka panyumba pake,+ koma wodana ndi ziphuphu ndi amene adzakhalebe ndi moyo.+ 28  Mtima wa munthu wolungama umayamba waganiza usanayankhe,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamasefukira zoipa.+ 29  Yehova amakhala kutali ndi anthu oipa,+ koma amamva pemphero la anthu olungama.+ 30  Maso+ owala amapangitsa mtima kusangalala.+ Uthenga+ wabwino umanenepetsa mafupa.+ 31  Munthu amene khutu lake limamvetsera chidzudzulo+ chopatsa moyo, amakhala pakati pa anthu anzeru.+ 32  Aliyense wokana malangizo+ amakana moyo wake, koma munthu womvetsera chidzudzulo amakhala ndi mtima wanzeru.+ 33  Kuopa Yehova ndi kumene kumaphunzitsa munthu kuchita zinthu mwanzeru,+ ndipo ulemerero umabwera pambuyo pa kudzichepetsa.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.