Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 11:1-31

11  Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova,+ koma mwala woyezera, wolemera mokwanira, umam’sangalatsa.  Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+  Mtima wosagawanika wa anthu owongoka ndi umene umawatsogolera,+ koma kupotoza zinthu kwa anthu ochita zachinyengo kudzawawononga.+  Zinthu zamtengo wapatali zidzakhala zopanda phindu pa tsiku la mkwiyo woopsa,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+  Kulungama kwa munthu wopanda cholakwa n’kumene kudzawongole njira yake,+ koma woipa adzagwera m’zoipa zakezo.+  Kulungama kwa anthu owongoka mtima n’kumene kudzawapulumutse,+ koma anthu ochita zinthu mwachinyengo adzagwidwa ndi zolakalaka zawo.+  Munthu woipa akafa, chiyembekezo chake chimawonongeka,+ ndipo zimene anali kuyembekezera kuchokera ku mphamvu zake sizichitika.+  Wolungama ndi amene amapulumutsidwa ku zowawa,+ ndipo woipa amalowa m’malo mwake.+  Wopanduka amawononga mnzake ndi pakamwa pake,+ koma anthu olungama amapulumutsidwa chifukwa chodziwa zinthu.+ 10  Mudzi umakondwera chifukwa cha makhalidwe abwino a anthu olungama,+ koma anthu oipa akawonongeka pamakhala mfuu yachisangalalo.+ 11  Mudzi umakwezedwa chifukwa cha madalitso a anthu olungama,+ koma umagwetsedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oipa.+ 12  Munthu wopanda nzeru mumtima mwake amanyoza mnzake,+ koma munthu wozindikira bwino ndi amene amakhala chete.+ 13  Amene amayendayenda n’kumanenera ena zoipa+ amaulula zinsinsi za anzake,+ koma wokhulupirika* amabisa nkhani.+ 14  Pakakhala popanda malangizo anzeru, anthu amagwa.+ Koma pakakhala aphungu ochuluka anthu amapulumuka.+ 15  Munthu amene walonjeza kuti adzapereka ngongole ya mlendo iye akadzalephera kubweza,+ zinthu sizidzamuyendera bwino. Koma wodana ndi kugwirana chanza pochita mgwirizano sakhala ndi nkhawa. 16  Mkazi wachikoka amapeza ulemu.+ Koma anthu ochitira nkhanza anzawo amapeza chuma. 17  Munthu wosonyeza kukoma mtima kosatha amapindulitsa moyo wake,+ koma munthu wankhanza amachititsa kuti thupi lake linyanyalidwe.+ 18  Munthu woipa amapeza malipiro achinyengo,+ koma wofesa chilungamo amapeza malipiro enieni.+ 19  Munthu wosasunthika pachilungamo adzapeza moyo,+ koma munthu wofunafuna zoipa adzafa.+ 20  Anthu a mtima wopotoka amam’nyansa Yehova,+ koma anthu opanda cholakwa m’njira yawo amam’sangalatsa.+ 21  Ngakhale dzanja ligwirane ndi dzanja linzake, munthu woipa sadzapewa chilango,+ koma ana a anthu olungama adzapulumuka ndithu.+ 22  Monga momwe chimakhalira chipini* chagolide pamphuno ya nkhumba, ndi mmenenso amakhalira mkazi wokongola koma wosaganiza bwino.+ 23  Zolakalaka za anthu olungama, ndithu n’zabwino.+ Chiyembekezo cha oipa chimabweretsa mkwiyo woopsa.+ 24  Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+ 25  Munthu wopatsa mowolowa manja adzalandira mphoto,+ ndipo wothirira ena mosaumira nayenso adzathiriridwa mosaumira.+ 26  Wokana kugulitsa mbewu zake kwa anthu, anthuwo adzam’temberera. Koma wolola kuzigulitsa adzalandira madalitso.+ 27  Wofunafuna kuchitira ena zabwino, amafunafuna kuvomerezedwa ndi Mulungu.*+ Koma wofunafuna kuchita zoipa, zoipazo zidzam’bwerera.+ 28  Wodalira chuma chake adzagwa,+ koma anthu olungama adzasangalala ngati masamba a zomera.+ 29  Aliyense wochititsa nyumba yake kunyanyalidwa+ adzagwira mphepo,+ ndipo munthu wopusa adzakhala wantchito wa munthu wa mtima wanzeru. 30  Zipatso za munthu wolungama ndizo mtengo wa moyo,+ ndipo munthu wopulumutsa miyoyo ndi wanzeru.+ 31  Wolungamatu adzalandira mphoto yake padziko lapansi.+ Ndiye kuli bwanji woipa ndi wochimwa?+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “wa mzimu wokhulupirika.”
“Chipini” ndi kachitsulo kapena kamtengo kokongoletsera kamene amakaika pabowo limene amaboola pamphuno.
Zingatanthauzenso kuvomerezedwa ndi anthu.