Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Miyambo 10:1-32

10  Miyambi ya Solomo.+ Mwana wanzeru amakondweretsa bambo ake,+ koma mwana wopusa amamvetsa chisoni mayi ake.+  Chuma cha anthu oipa chidzakhala chopanda phindu,+ koma chilungamo n’chimene chidzapulumutse munthu ku imfa.+  Yehova sadzachititsa munthu wolungama kukhala ndi njala,+ koma zolakalaka za anthu oipa adzazikankhira kumbali.+  Wogwira ntchito ndi dzanja laulesi adzakhala wosauka,+ koma dzanja la munthu wakhama ndi limene limalemeretsa.+  Mwana wozindikira amatuta m’chilimwe. Mwana wochititsa manyazi amakhala ali m’tulo tofa nato pa nthawi yokolola.+  Madalitso amapita pamutu pa wolungama,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+  Anthu akamakumbukira zabwino zimene munthu wolungama anali kuchita, amam’dalitsa,+ koma dzina la anthu oipa lidzawola.+  Munthu wanzeru mumtima mwake amamvera malamulo,+ koma wamilomo yopusa amaponderezedwa.+  Woyenda ndi mtima wosagawanika adzayenda popanda chomuopseza,+ koma wokhotetsa njira zake adzadziwika.+ 10  Wotsinzinira ena ndi diso lake adzamvetsa ena ululu,+ ndipo wamilomo yopusa adzaponderezedwa.+ 11  Pakamwa pa wolungama m’pamene pamachokera moyo,+ koma pakamwa pa anthu oipa pamabisa zachiwawa.+ 12  Chidani n’chimene chimayambitsa mikangano,+ koma chikondi chimaphimba machimo onse.+ 13  Pamilomo ya munthu womvetsa zinthu pamapezeka nzeru,+ koma ndodo amakwapulira msana wa munthu wopanda nzeru mumtima mwake.+ 14  Anzeru ndiwo amapitiriza kuphunzira zinthu zamtengo wapatali,+ koma pakamwa pa wopusa patsala pang’ono kuwonongeka.+ 15  Zinthu zamtengo wapatali za munthu wachuma zili ngati mudzi wake wolimba.+ Chiwonongeko cha onyozeka ndicho umphawi wawo.+ 16  Zochita za wolungama zimabweretsa moyo.+ Zokolola za woipa zimabweretsa tchimo.+ 17  Amene wagwira malangizo* mwamphamvu ndiye njira ya kumoyo,+ koma wosiya chidzudzulo amasocheretsa anthu.+ 18  Pamene pali munthu wobisa chidani pamakhala milomo yonyenga,+ ndipo wobweretsa uthenga woipa ndi wopusa.+ 19  Pakachuluka mawu sipalephera kukhala zolakwa,+ koma wodziwa kulamulira milomo yake amachita zinthu mwanzeru.+ 20  Lilime la wolungama ndilo siliva wabwino kwambiri.+ Mtima wa woipa ndi wopanda phindu.+ 21  Milomo ya wolungama imaweta anthu ambiri,+ koma zitsiru zimafa chifukwa chopanda nzeru mumtima.+ 22  Madalitso a Yehova ndi amene amalemeretsa,+ ndipo sawonjezerapo ululu.+ 23  Kwa wopusa, kusonyeza khalidwe lotayirira kuli ngati masewera,+ koma nzeru zimakhala ndi munthu wozindikira.+ 24  Chinthu choopsa kwa woipa n’chimene chidzamubwerere,+ koma anthu olungama adzapatsidwa zimene amalakalaka.+ 25  Woipa amatha ngati momwe zimakhalira pakawomba mphepo yamkuntho,+ koma wolungama ndiye maziko mpaka kalekale.*+ 26  Monga mmene amakhalira vinyo wowawasa m’mano ndiponso utsi m’maso, ndi mmenenso amakhalira munthu waulesi kwa amene am’tuma.+ 27  Kuopa Yehova kudzawonjezera masiku,+ koma zaka za anthu oipa zidzafupikitsidwa.+ 28  Zoyembekezera za olungama zimasangalatsa,+ koma chiyembekezo cha oipa chidzawonongeka.+ 29  Njira ya Yehova ndiyo malo achitetezo kwa munthu wopanda cholakwa,+ koma anthu ochita zopweteka ena adzawonongedwa.+ 30  Wolungama sadzagwedezedwa mpaka kalekale,+ koma anthu oipa sadzapitiriza kukhala padziko lapansi.+ 31  Pakamwa pa wolungama pamabala zipatso za nzeru,+ koma lilime lonena zopotoka lidzadulidwa.+ 32  Milomo ya wolungama imavomerezedwa ndi Mulungu,*+ koma pakamwa pa anthu oipa m’popotoka.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Miy 1:2.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Zingatanthauzenso kuvomerezedwa ndi anthu.