Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mika 7:1-20

7  Tsoka kwa ine,+ chifukwa ndakhala ngati munthu wanjala amene sanapeze zipatso kuti adye.+ Ndakhala ngati munthu amene sanapeze nkhuyu zoyambirira zimene anali kuzilakalaka, nthawi yokolola zipatso za m’chilimwe* ndi mphesa itatha.+  Anthu okhulupirika atha padziko lapansi, ndipo pakati pa anthu palibe munthu wowongoka mtima.+ Onse amadikirira anzawo kuti akhetse magazi.+ Aliyense amasaka m’bale wake ndi ukonde.+  Manja awo amachita zoipa ndipo amazichita bwino kwambiri.+ Kalonga amalamula kuti amupatse mphatso, ndipo woweruza amalandira chiphuphu poweruza.+ Munthu wotchuka amangolankhula zolakalaka za mtima wake+ ndipo onsewa amakonzera limodzi chiwembu.  Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati chitsamba chaminga, ndipo munthu wowongoka mtima kwambiri pakati pawo ndi woipa kwambiri kuposa mpanda wa mitengo yaminga.+ Tsiku limene mudzapatsidwe chilango, limene alonda anu ananena, lidzafika ndithu.+ Pa tsikulo anthu adzathedwa nzeru.+  Musamakhulupirire anzanu. Musamadalire mnzanu wapamtima.+ Samala zonena zako polankhula ndi amene umagona naye pafupi.+  Pakuti mwana wamwamuna akunyoza bambo ake. Mwana wamkazi akuukira mayi ake+ ndipo mkazi wokwatiwa akuukira apongozi ake aakazi.+ Adani ake a munthu ndi anthu a m’banja lake.+  Koma ine ndidzadikirira Yehova.+ Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.+ Mulungu wanga adzandimvera.+  Iwe mdani wanga,+ usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira. Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka ndithu.+ Ngakhale kuti ndili mumdima,+ Yehova adzakhala kuwala kwanga.+  Mkwiyo waukulu wa Yehova ndiupirira chifukwa ndamuchimwira.+ Ndiupirirabe kufikira ataweruza mlandu wanga mondikomera ndi kundichitira chilungamo.+ Iye adzandipititsa pamalo owala ndipo ndidzaona kulungama kwake.+ 10  Mdani wanga adzaona zimenezi, ndipo amene anali kunena kuti: “Yehova Mulungu wako ali kuti?”+ adzachita manyazi.+ Maso anga adzamuyang’ana.+ Iye adzakhala malo opondedwapondedwa ngati matope a mumsewu.+ 11  Pa tsiku lomanga mpanda wako wamiyala lamulo lokhudza iwe lidzachotsedwa.*+ 12  Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe kuchokera ku Asuri ndi kumizinda ya Iguputo. Anthu ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje*+ adzabwera kwa iwe. Adzabwera kuchokera m’malo onse apakati pa nyanja imodzi ndi nyanja ina, komanso pakati pa phiri limodzi ndi phiri lina.+ 13  Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha zochita za anthu okhala mmenemo ndi zotsatirapo za zochita zawozo.+ 14  Weta anthu ako ndi ndodo yako.+ Weta gulu la nkhosa zomwe ndi cholowa chako, zimene zinali kukhala zokhazokha m’nkhalango pakati pa mitengo ya zipatso.+ Uzilole kuti zikadyere ku Basana ndi ku Giliyadi+ ngati mmene zinali kuchitira masiku akale.+ 15  “Anthu inu ndidzakusonyezani zinthu zodabwitsa ngati mmene ndinachitira m’masiku amene munali kuchokera ku Iguputo.+ 16  Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ali ndi mphamvu.+ Adzagwira pakamwa+ ndipo makutu awo adzagontha. 17  Adzanyambita fumbi ngati njoka.+ Adzatuluka m’malo awo obisalamo+ ngati zokwawa zapadziko lapansi ali ndi mantha. Adzabwera kwa Yehova Mulungu akunjenjemera ndipo adzachita nanu mantha.”+ 18  Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu+ amene amakhululukira zolakwa+ ndi machimo a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+ Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale, pakuti kusonyeza kukoma mtima kosatha kumakusangalatsani.+ 19  Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzapondaponda zolakwa zathu.+ Machimo athu onse mudzawaponya pakati pa nyanja yozama.+ 20  Zonse zimene munanena kwa Yakobo zinali zoona ndipo Abulahamu munamusonyeza kukoma mtima kosatha. Ifenso mudzatichitira zomwezo chifukwa n’zimene munalonjeza makolo athu kalekale.+

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “zipatso za m’chilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.
Mawu ake enieni, “Pa tsikulo lamulo lidzakhala kutali.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.