Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mika 6:1-16

6  Anthu inu imvani zimene Yehova akunena.+ Nyamukani mukanene mlandu wanu kwa mapiri ndipo zitunda zikamve mawu anu.+  Inu mapiri, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake. Inu matanthwe okhazikika, tamverani. Mvetserani inu maziko a dziko lapansi, pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake. Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+  “Inu anthu anga,+ ndakulakwirani chiyani? Kodi ndakutopetsani mwa njira yanji?+ Perekani umboni wonditsutsa.+  Ine ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo, ndipo ndinakuwombolani m’nyumba ya akapolo. Ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.  Inu anthu anga, chonde kumbukirani zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha. Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu kukafika ku Giligala. Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”  Kodi nditenge chiyani popita kukakumana+ ndi Yehova? Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba?+ Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu ndi ana a ng’ombe achaka chimodzi?  Kodi Yehova adzakondwera ndi masauzande a nkhosa zamphongo? Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande makumimakumi?+ Kapena kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba kubadwa chifukwa cha cholakwa changa? Kodi ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?  Iwe munthu wochokera kufumbi, iye anakuuza zimene zili zabwino.+ Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima+ ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.  Mawu a Yehova akumveka mumzinda.+ Munthu wanzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu. Anthu inu, mverani mawu a ndodo ndi a amene anaisankha.+ 10  Kodi m’nyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo, ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wosaloleka? 11  Kodi ndingakhale woyera ndili ndi sikelo yachinyengo, ndiponso thumba lachinyengo lamiyala yoyezera zinthu? 12  Anthu olemera a mumzindawo amakonda kuchita zachiwawa. Anthu okhalamo akulankhula zonama+ ndipo lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.+ 13  “Ine ndidzakumenyani mpaka kukudwalitsani, ndipo mudzawonongedwa chifukwa cha machimo anu.+ 14  Inuyo mudzadya koma simudzakhuta ndipo mudzamvabe njala. Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino koma simudzatha kuziteteza. Zinthu zilizonse zimene mudzazitenge, ine ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.+ 15  Mudzabzala mbewu koma simudzakolola. Mudzaponda maolivi koma simudzadzola mafuta. Mudzaponda mphesa koma simudzamwa vinyo wotsekemera.*+ 16  Anthu inu mukutsatira zochita za Omuri. Zochita zonse za anthu a nyumba ya Ahabu, inunso mukuzichita ndipo mukuyendera maganizo awo.+ Pa chifukwa chimenechi ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa ndipo anthu a mumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+ Inuyo mudzatonzedwa ndi mitundu ina ya anthu.”+

Mawu a M'munsi

‘Muyezo wa efa’ ndi wofanana ndi chitini cha malita 22.
Ena amati “wonzuna.”