Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mika 3:1-12

3  Ine ndinapitiriza kunena kuti: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo ndi inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+ Kodi si inu oyenera kudziwa chilungamo?+  Inu mumadana ndi zinthu zabwino+ ndi kukonda zinthu zoipa.+ Mumasenda khungu la anthu ndi kuchotsa mnofu pamafupa awo.+  Mwadya mnofu wa anthu anga+ ndipo mwasenda khungu lawo. Mwaswa mafupa awo kukhala zidutswazidutswa. Mwawaphwanyaphwanya ngati mafupa ndi mnofu zimene zili mumphika wakukamwa kwakukulu komanso ngati nyama imene ili mumphika.+  Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize, koma sadzawayankha.+ Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo+ chifukwa cha zoipa zimene anali kuchita.+  “Yehova wanena zimene zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+ Aneneri amenewo akutafuna chakudya ndi mano awo+ n’kumanena kuti, ‘Mtendere!’+ Koma munthu akapanda kuika chakudya m’kamwa mwawo, amakonzekera kumuthira nkhondo.+ Kwa iwo Mulungu wanena kuti,  ‘Choncho anthu inu usiku udzakufikirani,+ ndipo simudzaonanso masomphenya.+ Mudzangoona mdima wokhawokha moti simudzaloseranso. Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera ndipo mdima udzawagwera masanasana.+  Oona masomphenya+ adzachita manyazi+ ndipo olosera+ adzakhumudwa ndithu. Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamlomo+ chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”+  Koma ine ndili ndi mphamvu zochuluka chifukwa cha mzimu wa Yehova. Ndine wokonzeka kuchita zachilungamo ndi kusonyeza mphamvu+ kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kupanduka kwawo, komanso kuti ndiuze Isiraeli za tchimo lake.+  Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo komanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+ amene mukuipidwa ndi chilungamo ndiponso amene mukupotoza chilichonse chowongoka.+ 10  Inu mukumanga Ziyoni ndi ntchito zokhetsa magazi ndipo mukumanga Yerusalemu mwa kuchita zinthu zopanda chilungamo.+ 11  Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+ 12  Chotero Ziyoni adzagawulidwa ngati munda chifukwa cha anthu inu ndipo Yerusalemu adzangokhala milu ya mabwinja.+ Phiri la nyumba ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda za m’nkhalango.

Mawu a M'munsi