Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 9:1-38

9  Chotero Yesu anakwera ngalawa n’kuwolokera tsidya lina, ndipo anapita kumzinda umene anali kukhala.+  Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pakabedi.+ Poona chikhulupiriro chawo, Yesu anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima, mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+  Atatero, alembi ena anang’ung’udza chamumtima kuti: “Munthu ameneyu akunyoza Mulungu.”+  Koma Yesu, podziwa zimene iwo anali kuganiza,+ ananena kuti: “N’chifukwa chiyani mukuganiza zinthu zoipa m’mitima mwanu?+  Mwachitsanzo, chapafupi n’chiti, kunena kuti, Machimo ako akhululukidwa, kapena kunena kuti, Nyamuka uyende?+  Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo+ . . .” pamenepo anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Nyamuka, tenga kabedi kakoka uzipita kwanu.”+  Ndipo ananyamuka n’kupita kwawo.  Khamu la anthulo litaona zimenezi, linagwidwa ndi mantha ndipo linatamanda Mulungu,+ amene anapereka mphamvu zimenezo+ kwa anthu.  Atachoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina wotchedwa Mateyu atakhala pansi mu ofesi yokhomera msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”+ Nthawi yomweyo ananyamuka ndi kum’tsatira.+ 10  Nthawi inayake, pamene anali kudya patebulo m’nyumba ina,+ kunabwera okhometsa msonkho ndi ochimwa ambiri ndipo anayamba kudya pamodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake. 11  Koma poona zimenezi, Afarisi anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?”+ 12  Iye atamva zimenezo, anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala,+ koma odwala ndi amene amamufuna. 13  Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” 14  Kenako ophunzira a Yohane anabwera kwa iye n’kumufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 15  Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa+ pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.+ 16  Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Pakuti mphamvu yonse ya chigambacho ingakoke ndi kung’amba malayawo ndipo kung’ambikako kungawonjezeke kwambiri.+ 17  Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka.+ Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano, ndipo zonse ziwirizo zimasungika bwino.”+ 18  Pamene anali kuwauza zimenezi, wolamulira wina+ anam’yandikira. Kenako anamugwadira+ n’kunena kuti: “Panopa mwana wanga wamkazi ayenera kuti wamwalira kale.+ Koma tiyeni mukamukhudze ndi dzanja lanu ndipo akhala ndi moyo.”+ 19  Pamenepo Yesu ananyamuka ndi kumutsatira. Ophunzira ake anachitanso chimodzimodzi. 20  Tsopano mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12 anafika kumbuyo kwake n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+ 21  chifukwa mumtima mwake anali kunena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” 22  Yesu anatembenuka, ndipo anaona mayiyo n’kunena kuti: “Mwanawe, limba mtima, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Kuchokera pa ola limenelo mayiyo anachira.+ 23  Tsopano atalowa m’nyumba ya wolamulira uja,+ anaona oliza zitoliro komanso khamu la anthu likubuma.+ 24  Yesu anawauza kuti: “Tulukani muno, pakuti mtsikanayu sanamwalire ayi, koma akugona.”+ Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kum’seka monyodola.+ 25  Atatulutsa anthu aja panja, iye analowa ndi kugwira dzanja la mtsikanayo,+ ndipo iye anadzuka.+ 26  Nkhani imeneyi inamveka m’dera lonselo. 27  Pamene Yesu anali kudutsa kuchokera kumeneko, anthu awiri akhungu+ anam’tsatira. Iwo anafuula ndi kunena kuti: “Mutichitire chifundo,+ Mwana wa Davide.” 28  Yesu atalowa m’nyumba, anthu akhunguwo anabwera kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi muli ndi chikhulupiriro+ kuti ndingachite zimenezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde, Ambuye.” 29  Kenako anawagwira m’maso,+ n’kunena kuti: “Malinga ndi chikhulupiriro chanu zichitike momwemo kwa inu,” 30  ndipo maso awo anatseguka. Chotero Yesu anawalamula mwamphamvu kuti: “Samalani, aliyense asadziwe zimenezi.”+ 31  Koma iwo, atatuluka kunja, anafalitsa za iye ponseponse m’dera limenelo.+ 32  Tsopano pamene iwo anali kunyamuka, anthu anam’bweretsera munthu wosalankhula wogwidwa ndi chiwanda.+ 33  Atatulutsa chiwandacho, munthu wosalankhulayo analankhula,+ moti khamu la anthulo linadabwa+ ndipo linanena kuti: “Zinthu zoterezi sizinaonekepo n’kale lonse mu Isiraeli.” 34  Koma Afarisi anayamba kunena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 35  Tsopano Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Anali kuphunzitsa m’masunagoge awo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda amtundu uliwonse ndi zofooka zilizonse.+ 36  Poona chikhamu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa. 37  Pamenepo anauza ophunzira ake kuti: “Inde, zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa.+ 38  Choncho pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.”+

Mawu a M'munsi