Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 7:1-29

7  “Lekani kuweruza ena+ kuti inunso musaweruzidwe,  pakuti chiweruzo chimene mukuweruza nacho ena inunso mudzaweruzidwa nacho.+ Ndipo muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.+  Nanga n’chifukwa chiyani umayang’ana kachitsotso m’diso la m’bale wako, koma osaganizira mtanda wa denga* la nyumba umene uli m’diso lako?+  Kapena ungauze bwanji m’bale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso m’diso lako,’ pamene iwe m’diso lako muli mtanda wa denga la nyumba?+  Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.  “Musamapatse agalu zinthu zopatulika,+ kapena kuponyera nkhumba ngale zanu, kuopera kuti zingapondeponde ngalezo+ kenako n’kutembenuka ndi kukukhadzulani.  “Pemphanibe,+ ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe,+ ndipo adzakutsegulirani.  Pakuti aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.  Inde, ndani pakati panu amene mwana wake+ atamupempha mkate, iye angamupatse mwala? 10  Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11  Chotero ngati inuyo, ngakhale kuti ndinu oipa,+ mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino+ kwa onse om’pempha! 12  “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni,+ inunso muwachitire zomwezo, pakuti n’zimene Chilamulo ndi Zolemba za aneneri zimafuna.+ 13  “Lowani pachipata chopapatiza.+ Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuchiwonongeko, ndipo anthu ambiri akuyenda mmenemo. 14  Koma chipata cholowera ku moyo n’chopapatiza komanso msewu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi owerengeka.+ 15  “Chenjerani ndi aneneri onyenga+ amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa,+ koma mkati mwawo ali mimbulu yolusa.+ 16  Mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+ Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamitula, amatero kodi?+ 17  Momwemonso mtengo uliwonse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabala zipatso zopanda pake.+ 18  Mtengo wabwino sungabale zipatso zopanda pake, ndiponso mtengo wovunda sungabale zipatso zabwino. 19  Mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino amaudula ndi kuuponya pamoto.+ 20  Chotero anthu amenewo mudzawazindikira ndi zipatso zawo.+ 21  “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wakumwamba ayi, koma yekhayo amene akuchita+ chifuniro cha Atate wanga wakumwamba.+ 22  Ambiri adzati kwa ine pa tsiku limenelo, ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere m’dzina lanu, ndi kutulutsa ziwanda m’dzina lanu, ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu m’dzina lanunso?’+ 23  Koma ine ndidzawauza momveka bwino kuti: Sindikukudziwani ngakhale pang’ono!+ Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.+ 24  “Chotero aliyense wakumva mawu angawa ndi kuwachita adzafanizidwa ndi munthu wochenjera, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.+ 25  Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo, koma sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. 26  Aliyense wakumva mawu angawa koma osawachita+ adzafanizidwa ndi munthu wopusa+ amene anamanga nyumba yake pamchenga. 27  Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinafika n’kuwomba nyumbayo+ moti inagwa, ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”+ 28  Tsopano Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa+ ndi kaphunzitsidwe kake, 29  chifukwa anali kuwaphunzitsa monga munthu waulamuliro,+ osati monga alembi awo.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “tsindwi.”