Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 5:1-48

5  Ataona khamu la anthu, anakwera m’phiri. Atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye.  Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:  “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu,+ chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.+  “Odala ndi anthu amene akumva chisoni, chifukwa adzasangalatsidwa.+  “Odala ndi anthu amene ali ofatsa,+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+  “Odala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo, chifukwa adzakhuta.+  “Odala ndi anthu achifundo,+ chifukwa adzachitiridwa chifundo.  “Odala ndi anthu oyera mtima,+ chifukwa adzaona Mulungu.+  “Odala ndi anthu amene amabweretsa mtendere,+ chifukwa adzatchedwa ‘ana+ a Mulungu.’ 10  “Odala ndi anthu amene akuzunzidwa+ chifukwa cha chilungamo, pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo. 11  “Ndinu odala pamene anthu akukunyozani+ ndi kukuzunzani,+ komanso kukunamizirani zoipa zilizonse chifukwa cha ine. 12  Kondwerani, dumphani ndi chimwemwe,+ chifukwa mphoto+ yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzira aneneri+ amene analipo inu musanakhaleko. 13  “Inu ndinu mchere+ wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yake angaibwezeretse motani? Sungagwire ntchito iliyonse koma ungafunike kuutaya kunja+ kumene anthu akaupondaponda. 14  “Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15  Anthu akayatsa nyale, saivundikira ndi dengu,+ koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse m’nyumbamo. 16  Momwemonso, onetsani kuwala+ kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino+ ndi kuti alemekeze+ Atate wanu wakumwamba. 17  “Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo+ kapena Zolemba za aneneri. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.+ 18  Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta,+ kusiyana n’kuti kalemba kochepetsetsa kapena kachigawo kamodzi ka lemba kachoke m’Chilamulo zinthu zonse zisanachitike.+ 19  Chotero aliyense wophwanya+ lililonse la malamulo aang’ono awa ndi kuphunzitsa anthu kuphwanya malamulowo, adzakhala ‘wosayenera kulowa’ mu ufumu wakumwamba.+ Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa,+ ameneyo adzakhala ‘woyenera kulowa’+ mu ufumu wakumwamba. 20  Pakuti ndikukuuzani inu kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha alembi ndi Afarisi,+ ndithudi simudzalowa+ mu ufumu wakumwamba. 21  “Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti ‘Usaphe munthu.+ Aliyense amene wapha mnzake+ wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ 22  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ m’bale wake wapalamula mlandu+ wa kukhoti. Komano aliyense wonenera m’bale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Ndipo aliyense wonena mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+ 23  “Choncho ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe,+ ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti m’bale wako ali nawe chifukwa,+ 24  siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako choyamba,+ ndipo ukabwerako, pereka mphatso yako.+ 25  “Thetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo+ asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wa pakhoti kuti akuponye m’ndende. 26  Kunena zoona, sudzatulukamo kufikira utalipira kakhobidi kotsirizira.+ 27  “Inu munamva kuti anati, ‘Usachite chigololo.’+   28  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyang’anitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo+ mumtima mwake.+ 29  Tsopano ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe+ m’Gehena. 30  Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya.+ Pakuti n’kwabwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana n’kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe m’Gehena. 31  “Pajanso anati, ‘Aliyense wothetsa ukwati+ ndi mkazi wake, apatse mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’+ 32  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wothetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha dama,*+ amamuchititsa chigololo akakwatiwanso,+ ndipo aliyense wokwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+ 33  “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+ 34  Koma ine ndikukuuzani kuti: Usamalumbire+ n’komwe, kutchula kumwamba, chifukwa ndi kumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu,+ 35  kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapena kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda+ wa Mfumu yaikulu. 36  Kapena usalumbire kutchula mutu wako, chifukwa sungathe kusandutsa ngakhale tsitsi limodzi kukhala loyera kapena lakuda. 37  Tangotsimikizani kuti mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi,+ pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.+ 38  “Inu munamva kuti anati, ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’+ 39  Koma ine ndikukuuzani kuti: Usalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenya mbama patsaya lakumanja,+ umutembenuzirenso linalo. 40  Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, m’patsenso akunja.+ 41  Winawake waudindo akakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire mtunda wa makilomita awiri.+ 42  Munthu akakupempha kanthu m’patse, ndipo munthu wofuna kukongola kanthu kwa iwe popanda chiwongoladzanja usamukanize.+ 43  “Inu munamva kuti anati, ‘Uzikonda mnzako+ ndi kudana ndi mdani wako.’+ 44  Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45  kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+ 46  Pakuti mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, kodi mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zimenezo? 47  Ngati mupatsa moni abale anu okha, kodi n’chiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48  Choncho khalani angwiro, monga mmene Atate wanu wakumwamba alili wangwiro.+

Mawu a M'munsi

 Onani Zakumapeto 6.
Mawu ake enieni, “limakupunthwitsa.”
Onani Zakumapeto 7.