Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 4:1-25

4  Kenako mzimu unatsogolera Yesu kuchipululu+ kuti akayesedwe+ ndi Mdyerekezi.  Atasala kudya masiku 40 usana ndi usiku,+ anamva njala.  Ndiyeno Woyesayo+ anabwera n’kumuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu,+ uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.”  Koma poyankha iye anati: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.’”*+  Kenako Mdyerekezi anamutenga ndi kupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi  n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi,+ pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, ndipo adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amatinso, ‘Usamuyese Yehova Mulungu wako.’”+  Ndiyeno Mdyerekezi anamutenganso ndi kupita naye paphiri lalitali kwambiri, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko+ ndi ulemerero wawo.  Kenako anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi+ ngati mutangogwada pansi n’kundiweramira kamodzi kokha.”+ 10  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira,+ ndipo uyenera kutumikira+ iye yekha basi.’”+ 11  Pamenepo Mdyerekezi uja anamusiya,+ ndipo kunabwera angelo ndi kuyamba kum’tumikira.+ 12  Tsopano Yesu atamva kuti Yohane amugwira,+ anachoka kumeneko ndipo anapita ku Galileya.+ 13  Komanso atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ n’kupeza malo okhala m’mphepete mwa nyanja m’zigawo za Zebuloni ndi Nafitali,+ 14  kuti mawu amene ananenedwa kudzera mwa Yesaya mneneri akwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 15  “Anthu okhala m’dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, m’mbali mwa msewu wa kunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya+ kumene kunali kukhala anthu a mitundu ina, 16  anthu okhala mu mdima+ anaona kuwala kwakukulu,+ ndipo anthu okhala m’dera la mthunzi wa imfa, kuwala+ kunawatulukira.”+ 17  Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira ndi kunena kuti: “Lapani+ anthu inu, pakuti ufumu+ wakumwamba wayandikira.” 18  Pamene anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba m’nyanja, pakuti anali asodzi. Mayina awo anali Simoni+ wotchedwa Petulo+ ndi Andireya. 19  Iye anawauza kuti: “Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 20  Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo+ n’kumutsatira. 21  Atapitirira pamenepo, anaona amuna enanso awiri+ apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi m’bale wake Yohane. Iwo anali m’ngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo,+ akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana. 22  Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo n’kumutsatira. 23  Atatero, anayendayenda+ m’Galileya+ yense kuphunzitsa m’masunagoge+ mwawo, kulalikira uthenga wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa anthu matenda amtundu uliwonse+ ndi zofooka zilizonse. 24  Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya+ monse. Anthu anamubweretsera onse amene sanali kumva bwino m’thupi,+ amene anali kuvutika ndi matenda komanso zowawa zamitundumitundu, ogwidwa ndi ziwanda, akhunyu,+ ndi anthu akufa ziwalo, ndipo iye anawachiritsa. 25  Chotero makamu a anthu ambiri ochokera ku Galileya,+ ku Dekapole, ku Yerusalemu,+ ku Yudeya komanso ochokera kutsidya lina la Yorodano, anam’tsatira.

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
M’Baibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete, komanso nyanja ya Tiberiyo.