Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 26:1-75

26  Tsopano Yesu atatsiriza kunena mawu onsewa, anauza ophunzira ake kuti:  “Inu mukudziwa kuti pasika achitika pakangopita masiku awiri,+ ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”+  Pa nthawiyi, ansembe aakulu ndiponso akulu anasonkhana m’bwalo lamkati kunyumba ya mkulu wa ansembe wotchedwa Kayafa.+  Iwo anali kupangana+ zoti agwire Yesu mochenjera ndi kumupha.  Koma anali kumangonena kuti: “Tisadzamugwire pa chikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”+  Pamene Yesu anali ku Betaniya+ m’nyumba ya Simoni wakhate,+  kunafika mayi wina ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala muli mafuta onunkhira okwera mtengo.+ Mayiyo atayandikira Yesu, anayamba kumuthira mafutawo m’mutu pamene iye anali kudya patebulo.  Ophunzira ake ataona zimenezi anakwiya n’kunena kuti: “N’kuwonongeranji chonchi?+  Mafuta amenewa akanagulitsidwa ndalama zambiri ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka.”+ 10  Yesu anadziwa zimenezi,+ ndipo anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+ 11  Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 12  Pakuti pamene mayiyu wathira mafuta onunkhirawa pathupi langa chonchi, wachita zimenezi kukonzekera kuikidwa kwanga m’manda.+ 13  Ndithu ndikukuuzani, Kulikonse kumene uthenga wabwinowu udzalalikidwe m’dziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzam’kumbukira.”+ 14  Pambuyo pake mmodzi wa ophunzira 12 aja, wotchedwa Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu 15  n’kuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+ 16  Choncho kuchokera pamenepo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino umene angamuperekere.+ 17  Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha mikate yopanda chofufumitsa,+ ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako pasika?”+ 18  Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti+ ndipo mukamuuze kuti, Mphunzitsi wanena kuti, ‘Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.’”+ 19  Chotero ophunzirawo anachitadi monga mmene Yesu anawalamulira, ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa pasika.+ 20  Nthawi yamadzulo,+ iye ndi ophunzira ake 12 aja anali kudya chakudya patebulo.+ 21  Pamene anali kudya, iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, Mmodzi wa inu andipereka.”+ 22  Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?”+ 23  Poyankha iye anati: “Amene akusunsa nane limodzi m’mbalemu ndi amene ati andipereke.+ 24  Zoona, Mwana wa munthu akuchokadi, monga Malemba amanenera+ za iye, koma tsoka+ kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.” 25  Poyankha, Yudasi amene anali atatsala pang’ono kumupereka anati: “Nanga n’kukhala ine Rabi?” Iye anati: “Wanena wekha.” 26  Pamene anali kudya, Yesu anatenga mkate,+ ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema+ n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: “Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 27  Kenako anatenga kapu+ ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: “Imwani nonsenu.+ 28  Vinyoyu akuimira+ ‘magazi+ anga a pangano,’+ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri+ kuti machimo akhululukidwe.+ 29  Koma ndikukuuzani kuti, kuyambira tsopano sindidzamwanso chakumwa ichi chochokera ku mphesa kufikira tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano limodzi ndi inu mu ufumu wa Atate wanga.”+ 30  Potsirizira pake, atatha kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,+ anatuluka n’kupita kuphiri la Maolivi.+ 31  Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa ndi kundisiya ndekha usiku uno, pakuti Malemba amati, ‘Ndidzapha m’busa, ndipo nkhosa za m’gululo zidzabalalika.’+ 32  Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 33  Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!”+ 34  Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe, Usiku womwe uno tambala asanalire, undikana katatu.”+ 35  Petulo anayankha kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ophunzira ena onse ananenanso chimodzimodzi.+ 36  Kenako Yesu anafika nawo pamalo+ otchedwa Getsemane, ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphera.”+ 37  Popita kumeneko anatenga Petulo ndi ana awiri+ a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 38  Kenako anawauza kuti: “Moyo wanga ukumva chisoni chofa nacho.+ Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+ 39  Choncho atapita patsogolo pang’ono, anagwada mpaka nkhope yake pansi, ndipo anapemphera+ kuti: “Atate wanga, ngati n’kotheka, kapu+ iyi indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga,+ koma mwa kufuna kwanu.”+ 40  Atatero anabwerera pamene panali ophunzira ake aja ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Zoona anthu inu simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine ola limodzi?+ 41  Khalani maso+ ndipo pempherani+ kosalekeza kuti musalowe m’mayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 42  Anachokanso kachiwiri+ n’kupita kukapemphera kuti: “Atate wanga, ngati sizingatheke kuti kapuyi indipitirire mpaka nditamwa ndithu, chifuniro chanu chichitike.”+ 43  Anabwerera n’kuwapezanso akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera.+ 44  Choncho anawasiya ndi kupitanso kukapemphera kachitatu,+ kubwereza mawu omwe aja. 45  Pambuyo pake anabwerera kwa ophunzirawo n’kuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula! Taonani! Ola lakuti Mwana wa munthu aperekedwe m’manja mwa ochimwa layandikira.+ 46  Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+ 47  Mawu adakali m’kamwa, Yudasi,+ mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi khamu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga+ ndi zibonga.+ 48  Apa n’kuti womupereka ameneyu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndim’psompsone ndi ameneyo, mum’gwire.”+ 49  Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu n’kunena kuti: “Mtendere ukhale nanu Rabi!”+ Ndipo anam’psompsona.+ 50  Koma Yesu+ anamufunsa kuti: “Bwanawe, ukupezeka kuno ndi cholinga chotani?” Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu ndi kum’manga.+ 51  Koma wina mwa amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 52  Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako m’chimake,+ pakuti onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.+ 53  Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+ 54  Koma ndikachita zimenezo, nanga Malemba amene ananeneratu kuti izi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” 55  Mu ola lomwelo Yesu anafunsa khamu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukukalimbana ndi wachifwamba?+ Tsiku ndi tsiku ndinali kukhala pansi m’kachisi+ ndi kuphunzitsa, koma simunandigwire. 56  Koma zonsezi zachitika kuti malemba a aneneri akwaniritsidwe.”+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa, n’kumusiya yekha.+ 57  Amene anagwira Yesu aja anapita naye kwa Kayafa+ mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anali atasonkhana.+ 58  Koma Petulo anali kumutsatirabe chapatali ndithu, mpaka anafika m’bwalo lamkati+ kunyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkatimo, anakhala pansi pamodzi ndi antchito a m’nyumbamo kuti aone zotsatira zake.+ 59  Pa nthawiyi ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* anali kufunafuna umboni wonama kuti amunamizire mlandu Yesu ndi kumupha+ 60  koma sanaupeze, ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zonama.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri 61  ndi kunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu ndi kumumanganso m’masiku atatu.’”+ 62  Pamenepo mkulu wa ansembe anaimirira ndi kumufunsa kuti: “Kodi ukusowa choyankha? Kodi n’zoona zimene awa akukunenezazi?”+ 63  Koma Yesu anangokhala chete.+ Chotero mkulu wa ansembe anati: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo,+ utiuze ngati ndiwedi Khristu+ Mwana wa Mulungu!” 64  Yesu anamuyankha+ kuti: “Mwanena nokha.+ Ndipo ndikukuuzani anthu inu kuti, kuyambira tsopano+ mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+ 65  Pamenepo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake akunja n’kunena kuti: “Wanyoza Mulungu!+ Nanga n’kufunanso mboni zina pamenepa?+ Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu.+ 66  Tsopano inu mukuona bwanji pamenepa?” Iwo anayankha kuti: “Ayenera kuphedwa basi.”+ 67  Kenako anayamba kumulavulira kunkhope+ ndi kum’menya+ nkhonya. Ena anamuwomba mbama,+ 68  ndi kunena kuti: “Losera tione Khristu iwe.+ Wakumenya ndani?”+ 69  Tsopano Petulo anakhala pansi m’bwalo lamkati, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye n’kunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!”+ 70  Koma iye anakana pamaso pa onse kuti: “Sindikudziwa zimene ukunena.” 71  Atatuluka n’kupita kukanyumba kapachipata, mtsikana wina anamuzindikira ndi kuuza ena amene anali pafupi kuti: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.”+ 72  Apanso Petulo anakana mochita kulumbira ndipo ananena kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!”+ 73  Patapita kanthawi pang’ono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera ndi kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli m’gulu la ophunzira ake. Ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.”+ 74  Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Nthawi yomweyo tambala analira.+ 75  Tsopano Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja, akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja n’kuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”