Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 23:1-39

23  Pambuyo pake Yesu analankhula kwa khamu la anthu ndi kwa ophunzira ake+ kuti:  “Alembi+ ndi Afarisi adzikhazika pampando wa Mose.  Chotero muzichita ndi kutsatira zilizonse zimene angakuuzeni,+ koma musamachite zimene iwo amachita,+ chifukwa iwo amangonena koma osachita.  Iwo amamanga akatundu olemera ndi kusenzetsa anthu pamapewa,+ koma eni akewo safuna kusuntha akatunduwo ndi chala chawo.+  Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone.+ Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera, ndipo amakulitsanso ulusi wopota wa m’mphepete mwa zovala zawo.  Amakonda malo olemekezeka kwambiri+ pa chakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo m’masunagoge.+  Amakondanso kupatsidwa moni+ m’misika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.+  Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha,+ ndipo nonsenu ndinu abale.  Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, pakuti Atate wanu ndi mmodzi,+ wakumwamba Yekhayo. 10  Musamatchedwe ‘atsogoleri,’+ pakuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. 11  Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.+ 12  Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa,+ koma aliyense wodzichepetsa adzakwezedwa.+ 13  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mukutseka+ ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Pakuti inuyo+ simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe. 14 * —— 15  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenera kuponyedwa m’Gehena* kuposa inuyo. 16  “Tsoka kwa inu atsogoleri akhungu,+ amene mumati, ‘Ngati munthu walumbirira kachisi palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira golide wa m’kachisi, asunge lumbiro lake.’+ 17  Opusa ndi akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, golide kapena kachisi amene wayeretsa golideyo? 18  Komanso mumati, ‘Ngati munthu walumbirira guwa lansembe, palibe kanthu, koma ngati munthu walumbirira mphatso imene ili paguwapo, asunge lumbiro lake.’ 19  Akhungu inu! Chofunika kwambiri n’chiti, mphatso kapena guwa lansembe limene limayeretsa mphatsoyo? 20  Chotero amene walumbirira guwa lansembe walumbirira guwalo ndi zonse zimene zili pamenepo, 21  ndipo amene walumbirira kachisi walumbirira kachisiyo limodzi ndi iye amene amakhala mmenemo. 22  Wolumbirira kumwamba walumbirira mpando wachifumu wa Mulungu+ komanso amene akukhala pampandowo. 23  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili, ndi chitowe, koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika.+ Kupereka zinthu zimenezi n’kofunikadi, koma osanyalanyaza zinthu zinazo. 24  Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere koma mumameza ngamila. 25  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Chifukwa mumayeretsa kunja kwa kapu+ ndi mbale, koma mkati mwake mutadzaza zolanda+ ndi kusadziletsa. 26  Mfarisi wakhungu+ iwe, yeretsa mkati mwa kapu+ ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera. 27  “Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu, amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28  Mofanana ndi zimenezi inunso, pamaso pa anthu, mumaonekadi ngati olungama+ koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo. 29  “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda achikumbutso a anthu olungama,+ 30  ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’+ 31  Chotero mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+ 32  Choncho malizitsani ntchito+ imene makolo anu anayamba. 33  “Njoka inu, ana a mphiri, mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?+ 34  Pa chifukwa chimenechi, tsopano ndikukutumizirani+ aneneri, anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ ndi kuwapachika, ndipo ena mudzawakwapula+ m’masunagoge mwanu ndi kuwazunza mumzinda ndi mzinda, 35  kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu,+ kuyambira magazi a Abele+ wolungama mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe. 36  Ndithu ndikukuuzani kuti, Zinthu zonsezi zidzaubwerera m’badwo uwu. 37  “Yerusalemu, Yerusalemu, wakupha aneneri iwe+ ndi woponya miyala+ anthu otumizidwa kwa iwe. Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, muja nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko.+ Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 38  Tsopano tamverani! Mulungu wachoka n’kukusiyirani+ nyumba* yanuyi. 39  Ndithu ndikukuuzani, Kuyambira tsopano simudzandionanso kufikira pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa iye wobwera m’dzina la Yehova!’”+

Mawu a M'munsi

Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 6.
Kutanthauza kachisi.