Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Mateyu 22:1-46

22  Popitiriza kuwayankha, Yesu anawauzanso mafanizo ena kuti:+  “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonza phwando la ukwati wa mwana wake.  Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa ku phwando laukwati,+ koma anthuwo sanafune kubwera.+  Kenako inatumanso akapolo ena+ kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ng’ombe zanga komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani ku phwando laukwati.”’+  Koma anthuwo ananyalanyaza ndi kuchoka. Wina anapita kumunda wake, wina kumalonda ake.+  Koma enawo anagwira akapolo akewo, ndi kuwachitira zachipongwe n’kuwapha.+  “Pamenepo mfumu ija inakwiya kwambiri, ndipo inatumiza asilikali ake kukawononga opha anthu amenewo ndi kutentha mzinda wawo.+  Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa ndithu, koma oitanidwa aja anali osayenera.+  Chotero pitani m’misewu yotuluka mumzinda, ndipo aliyense amene mukam’peze, mukamuitanire phwando laukwatili.’+ 10  Choncho akapolowo anapita m’misewu ndi kusonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe.+ Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu oyembekezera kulandira chakudya.+ 11  “Pamene mfumu ija inalowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati.+ 12  Chotero inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’+ Iye anasowa chonena. 13  Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘M’mangeni manja ndi miyendo ndipo mum’ponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’+ 14  “Pakuti oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”+ 15  Pamenepo Afarisi anachoka ndi kukapangana kuti am’kole m’mawu ake.+ 16  Choncho anamutumizira ophunzira awo, limodzi ndi achipani cha Herode,+ ndipo iwo anati: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu m’choonadi, ndiponso simusamala kuti uyu ndani, chifukwa simuyang’ana maonekedwe a anthu.+ 17  Ndiye tatiuzani, Mukuganiza bwanji? Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+ 18  Koma Yesu, podziwa kuipa mtima kwawo, ananena kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa?+ 19  Ndionetseni khobidi la msonkho.” Pamenepo anam’bweretsera khobidi limodzi la dinari. 20  Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi ndi mawu akewa n’zandani?”+ 21  Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Pamenepo iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu, kwa Mulungu.”+ 22  Atamva zimenezi, anadabwa ndipo anangochokapo n’kumusiya.+ 23  Pa tsikulo Asaduki, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa iye n’kumufunsa kuti:+ 24  “Mphunzitsi, Mose anati, ‘Ngati munthu wamwalira wopanda ana, m’bale wake ayenera kukwatira mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana.’ 25  Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako n’kumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkazi uja anakwatiwa ndi m’bale wa mwamuna wake.+ 26  Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja.+ 27  Pamapeto pake mkaziyo nayenso anamwalira. 28  Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+ 29  Koma Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.+ 30  Pakuti pouka kwa akufa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa,+ koma adzakhala ngati angelo akumwamba. 31  Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti,+ 32  ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’? Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.”+ 33  Pakumva zimenezo, khamu la anthulo linadabwa ndi zimene anali kuphunzitsa.+ 34  Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa chonena Asaduki, anasonkhana monga gulu limodzi. 35  Ndipo mmodzi wa iwo, wodziwa Chilamulo,+ anafunsa Yesu momuyesa kuti: 36  “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri m’Chilamulo ndi liti?”+ 37  Iye anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova* Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ 38  Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. 39  Lachiwiri lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’ 40  Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso Zolemba za aneneri.”+ 41  Tsopano Afarisi aja atasonkhana pamodzi Yesu anawafunsa kuti:+ 42  “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+ 43  Iye anawafunsanso kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu, Davide anamutcha ‘Ambuye,’ muja anati, 44  ‘Yehova wauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako kunsi kwa mapazi ako”’?+ 45  Chotero ngati Davide anamutcha kuti ‘Ambuye,’ akukhala bwanji mwana wake?”+ 46  Koma panalibe ngakhale mmodzi amene anatha kumuyankha, ndipo kuchokera tsiku limenelo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.