Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 99:1-9

99  Yehova wakhala mfumu.+ Mitundu ya anthu inthunthumire.+ Iye wakhala pa akerubi.+ Ndipo dziko lapansi linjenjemere.+   Yehova wasonyeza mu Ziyoni kuti ndi wamkulu,+ Ndipo ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+   Iwo atamande dzina lanu.+ Dzina lanu ndi lalikulu, lochititsa mantha ndi loyera.+   Iye amakonda chilungamo ngati mmene mfumu yamphamvu imachitira.+ Inu mwakhazikitsa kulungama.+ Mwakhazikitsa chiweruzo ndi chilungamo pakati pa ana a Yakobo.+   Kwezani Yehova Mulungu wathu+ ndipo muweramireni pachopondapo mapazi ake.+ Iye ndi woyera.+   Mose ndi Aroni anali pakati pa ansembe ake,+ Samueli anali pakati pa anthu amene anali kuitana pa dzina lake.+ Iwo anali kuitana Yehova, ndipo iye anali kuwayankha.+   Mulungu anapitiriza kulankhula nawo mumtambo woima njo ngati chipilala.+ Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malangizo amene anawapatsa.+   Inu Yehova Mulungu wathu munawayankha.+ Kwa iwo munasonyeza kuti ndinu Mulungu wokhululuka,+ Ndiponso wopereka chilango chifukwa cha zochita zawo zoipa.+   Kwezani Yehova Mulungu wathu,+ Ndipo weramani paphiri lake loyera.+ Pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.+

Mawu a M'munsi