Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 98:1-9

Nyimbo. 98  IMBIRANI Yehova nyimbo yatsopano,+ Pakuti zimene wachita ndi zodabwitsa.+ Dzanja lake lamanja, ndithu mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.+   Yehova wachititsa chipulumutso chake kudziwika.+ Chilungamo chake wachisonyeza ku mitundu ya anthu.+   Iye wakumbukira lonjezo lake losonyeza kukoma mtima kosatha ndi kukhulupirika kwake ku nyumba ya Isiraeli.+ Malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu.+   Fuulirani Yehova mosangalala chifukwa wapambana, inu nonse anthu a padziko lapansi.+ Kondwerani, fuulani mosangalala ndi kuimba nyimbo zomutamanda.+   Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda ndi zeze,+ Muimbireni nyimbo ndi zeze ndi kumutamanda ndi nyimbo zokoma.+   Fuulani mwa kuimba malipenga ndi mphalasa.*+ Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova, chifukwa wapambana.   Nyanja ndi zonse zili mmenemo zichite mkokomo,+ Chimodzimodzinso mtunda ndi zonse zokhala kumeneko.+   Mitsinje iwombe m’manja, Mapiri onse afuule pamodzi mokondwera pamaso pa Yehova.+   Pakuti iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+ Adzaweruza dziko mwachilungamo,+ Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu molungama.+

Mawu a M'munsi

“Mphalasa” ndi lipenga lopangidwa ndi nyanga ya nkhosa.