Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 97:1-12

97  Yehova wakhala mfumu!+ Dziko lapansi likondwere,+ Ndipo zilumba zambiri zisangalale.+   Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+ Chilungamo ndi chiweruzo ndizo malo okhazikika a mpando wake wachifumu.+   Patsogolo pake pakuyaka moto,+ Ndipo ukupsereza adani ake onse omuzungulira.+   Mphezi zake zinawalitsa dziko lapansi.+ Dziko linaona ndipo linachita mantha kwambiri.+   Mapiri anasungunuka ngati phula chifukwa cha Yehova,+ Chifukwa cha Ambuye wa dziko lonse lapansi.+   Kumwamba kwalengeza za chilungamo chake,+ Ndipo mitundu yonse ya anthu yaona ulemerero wake.+   Onse amene akupembedza chifaniziro chilichonse achite manyazi.+ Amene amadzitama chifukwa cha milungu yopanda pake achite manyazi.+ Muweramireni, inu milungu yonse.+   Ziyoni anamva ndipo anayamba kusangalala,+ Midzi yozungulira Yuda inayamba kukondwera+ Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+   Pakuti inu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba wolamulira dziko lonse lapansi.+ Mwakwera pamwamba kwambiri kuposa milungu ina yonse.+ 10  Inu okonda Yehova+ danani nacho choipa.+ Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+ Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.+ 11  Kuwala kwaunikira wolungama,+ Ndipo anthu owongoka mtima akusangalala.+ 12  Sangalalani chifukwa cha Yehova, anthu olungama inu,+ Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “chikumbutso chake choyera.”