Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 96:1-13

96  Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+ Imbirani Yehova, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+   Imbirani Yehova, tamandani dzina lake.+ Tsiku ndi tsiku lengezani uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+   Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,+ Ndiponso ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+   Pakuti Yehova ndi wamkulu+ ndi woyenera kutamandidwa kwambiri. Iye ndi wochititsa mantha kuposa milungu ina yonse.+   Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+ Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+   Ulemu ndi ulemerero zili pamaso pake.+ Mphamvu ndi kukongola zili m’nyumba yake yopatulika.+   Vomerezani Yehova, inu mabanja a mitundu ya anthu,+ M’patseni Yehova ulemerero ndi kuvomereza kuti iye ndi wamphamvu.+   M’patseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+ Tengani mphatso ndi kulowa m’mabwalo ake.+   Gwadirani Yehova mutavala zovala zokongola ndi zopatulika.+ Njenjemerani ndi mantha aakulu* pamaso pake, inu anthu nonse okhala padziko lapansi.+ 10  Nenani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala mfumu.+ Dziko lapansi nalonso lakhazikika moti silingagwedezeke.+ Iye adzaweruzira mitundu ya anthu milandu yawo mwachilungamo.”+ 11  Kumwamba kukondwere, ndipo dziko lapansi lisangalale.+ Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo.+ 12  Mtunda ukondwere ndi zonse zimene zili kumeneko.+ Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo ya m’nkhalango ifuule mokondwera pamaso pa Yehova.+ 13  Pakuti iye wabwera.+ Iye wabwera kudzaweruza dziko lapansi.+ Adzaweruza dziko mwachilungamo,+ Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “imvani kupweteka kwambiri.”