Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 95:1-11

95  Bwerani tifuule kwa Yehova mokondwera!+ Iye amene ndi Thanthwe la chipulumutso chathu, timufuulire mosangalala chifukwa wapambana.+   Tiyeni tionekere pamaso pake ndi chiyamiko.+ Tiyeni tiimbe nyimbo zomutamanda ndi kumufuulira mosangalala chifukwa wapambana.+   Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,+ Ndiponso ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+   Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali m’manja mwake,+ Mapiri aatali nawonso ndi ake.+   Nyanja imene anapanga ndi yake,+ Iye amenenso anapanga mtunda ndi manja ake.+   Bwerani timuweramire ndi kumupembedza.+ Tiyeni tigwade+ pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga.+   Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.+ Lero anthu inu mukamvera mawu a Mulungu,+   Musaumitse mitima yanu monga mmene makolo anu anachitira pa Meriba,+ Monga mmene anachitira pa Masa m’chipululu,+   Pamene makolo anu anandiyesa.+ Iwo anandisanthula, ndipo anaonanso ntchito zanga.+ 10  Kwa zaka 40, m’badwo umenewo unali kundinyansa,+ Ndipo ndinati: “Anthu awa mitima yawo imasochera,+ Ndipo sadziwa njira zanga.”+ 11  Kunena za anthu amenewa ndinalumbira mu mkwiyo wanga kuti:+ “Sadzalowa mu mpumulo wanga.”+

Mawu a M'munsi