Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 94:1-23

94  Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+ Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+   Nyamukani inu Woweruza dziko lapansi.+ Perekani chilango kwa anthu odzikweza.+   Kodi anthu oipa adzakondwera kufikira liti?+ Kodi adzakondwera kufikira liti, inu Yehova?+   Iwo amalankhula zopanda pake, ndipo amalankhula mosasamala.+ Onse ochita zopweteka anzawo amadzitukumula.+   Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+ Ndipo amasautsa cholowa chanu.+   Amapha mkazi wamasiye ndi mlendo wokhala m’dziko lawo,+ Ndipo amaphanso ana amasiye.*+   Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+ Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+   Zindikirani anthu opanda nzeru inu.+ Ndipo opusa inu, mudzakhala liti ozindikira?+   Kodi amene anakupatsani makutu, sangamve?+ Kapena amene anapanga maso, sangaone?+ 10  Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu,+ Amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira, sangathe kudzudzula?+ 11  Yehova amadziwa kuti maganizo a anthu ali ngati mpweya wotuluka m’mphuno.+ 12  Wodala ndi munthu wamphamvu amene inu Ya mumamudzudzula,+ Komanso amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+ 13  Kuti mum’patse mtendere pa nthawi ya masoka,+ Kufikira dzenje la munthu woipa litakumbidwa.+ 14  Yehova sadzataya anthu ake,+ Kapena kusiya cholowa chake.+ 15  Pakuti zigamulo zidzayambiranso kukhala zachilungamo,+ Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira. 16  Ndani adzanyamuka kuti amenye nkhondo ndi anthu ochita zoipa m’malo mwa ine?+ Ndani adzaima m’malo mwa ine kulimbana ndi anthu ochita zopweteka anzawo?+ 17  Yehova akanapanda kundithandiza,+ Ndikanatsikira kuli chete mofulumira.+ 18  Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa literereka,”+ Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandichirikiza.+ 19  Malingaliro osautsa atandichulukira mumtima mwanga,+ Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.+ 20  Kodi inu mudzagwirizana ndi olamulira ankhanza,+ Pamene akuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo?+ 21  Iwo amaukira koopsa munthu wolungama,+ Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti ndi woipa. Amachita zimenezi kuti akhetse magazi ake.+ 22  Koma Yehova adzakhala malo anga okwezeka ndiponso achitetezo,+ Ndipo Mulungu wanga adzakhala thanthwe langa lothawirako.+ 23  Iye adzawabwezera zoipa zawo,+ Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+ Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”