Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 93:1-5

93  Yehova wakhala mfumu!+ Iye wavala ulemerero.+ Yehova wavala mphamvu ngati chovala, ndipo wamangirira mphamvuzo m’chiuno mwake.+ Dziko lapansi lakhazikika, moti silingagwedezeke.+   Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+ Munakhalako kuyambira kalekale.+   Inu Yehova, mitsinje ikufuula. Ikufuula ndi mawu amphamvu.+ Mitsinje ikupitiriza kufuula ndi mawu amkokomo.+   Ulemerero wa Yehova ndi waukulu+ kumwamba, Kuposa mkokomo wa madzi ambiri, kuposanso mafunde amphamvu a m’nyanja.+   Zikumbutso zanu ndi zodalirika zedi.+ Chiyero ndi choyenera nyumba yanu+ mpaka muyaya, inu Yehova.+

Mawu a M'munsi