Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 92:1-15

Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la sabata. 92  Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+ Ndi kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wam’mwambamwamba.+   Ndi bwino kunena za kukoma mtima kwanu kosatha m’mawa,+ Ndi za kukhulupirika kwanu usiku,+   Ndipo ndidzatero pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu.+ Ndidzaimba nyimbo yomveka bwino ndi zeze.+   Pakuti mwandichititsa kusangalala, inu Yehova, chifukwa cha zochita zanu. Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito ya manja anu.+   Ntchito zanu ndi zazikuludi inu Yehova!+ Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+   Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,+ Ndipo munthu wopusa sangazimvetse.+   Anthu oipa akamaphuka ngati msipu,+ Ndipo anthu onse ochita zopweteka anzawo akamaphuka ngati maluwa, Amatero kuti awonongeke kwamuyaya.+   Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.+   Pakuti taonani adani anu, inu Yehova!+ Adani anu onse adzatha!+ Anthu onse ochita zopweteka anzawo adzamwazikana.+ 10  Koma inu mudzakweza nyanga* yanga ngati nyanga ya ng’ombe yam’tchire yamphongo.*+ Ndidzadzola mafuta abwino.+ 11  Diso langa lidzayang’ana adani anga atagonja,+ Makutu anga adzamva za anthu ondiukira, anthu ochita zoipa. 12  Wolungama adzakula ngati mtengo wa kanjedza,+ Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+ 13  Anthu obzalidwa m’nyumba ya Yehova,+ M’mabwalo a Mulungu wathu,+ adzakula mosangalala. 14  Zinthu zidzapitiriza kuwayendera bwino ngakhale atachita imvi,+ Adzakhalabe onenepa ndi athanzi,+ 15  Kuti alengeze kuti Yehova ndi wolungama.+ Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.