Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 91:1-16

91  Aliyense wokhala m’malo otetezeka+ a Wam’mwambamwamba+ Adzakhala wosungika mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+   Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo,+ Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+   Pakuti iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,+ Ndi ku mliri wobweretsa masautso.+   Adzakutchinjiriza ndi mapiko ake,+ Udzathawira pansi pa mapiko ake.+ Choonadi chake+ chidzakhala chishango chako+ chachikulu ndi malo ako achitetezo.   Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+ Ndipo sudzaopanso muvi+ woponyedwa masana,   Sudzaopa mliri umene umayenda mu mdima,+ Kapena chiwonongeko chimene chimachitika dzuwa lili paliwombo.+   Anthu 1,000 adzagwa pambali pako, Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja. Koma palibe zoterezi zimene zidzakuchitikira.+   Udzayang’ana ndi maso ako,+ Ndipo udzaona anthu oipa akulandira chilango.+   Popeza wanena kuti: “Yehova ndiye pothawirapo panga,”+ Wapanga Wam’mwambamwamba kukhala malo ako okhalamo.+ 10  Palibe tsoka limene lidzakugwera,+ Ndipo ngakhale mliri sudzayandikira hema wako.+ 11  Pakuti adzalamula angelo ake za iwe,+ Kuti akuteteze m’njira zako zonse.+ 12  Iwo adzakunyamula m’manja mwawo,+ Kuti phazi lako lisawombe mwala uliwonse.+ 13  Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,+ Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri ndi chinjoka.+ 14  Mulungu wanena kuti: “Popeza wasonyeza kuti amandikonda,+ Inenso ndidzamupulumutsa.+ Ndidzamuteteza chifukwa wadziwa dzina langa.+ 15  Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+ Ndidzakhala naye m’nthawi ya masautso.+ Ndidzamupulumutsa ndi kumupatsa ulemerero.+ 16  Ndidzamukhutiritsa ndi masiku ambiri,+ Ndipo ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Mawu a M'munsi