Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 89:1-52

Masikili.* Salimo la Etani wa m’banja la Zera.+ 89  Ndidzaimba mpaka kalekale za ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha.+ Ndidzalengeza ndi pakamwa panga ku mibadwomibadwo za kukhulupirika kwanu.+   Pakuti ndanena kuti: “Kukoma mtima kwanu kosatha kudzakhazikika mpaka kalekale.+ Ndipo mwakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba.”+   Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+ Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga,+   ‘Ndidzakhazikitsa mbewu yako mpaka kalekale,+ Ndipo ndidzalimbitsa  mpando wako wachifumu+ ku mibadwomibadwo.’” [Seʹlah.]   Inu Yehova, kumwamba kudzatamanda ntchito zanu zodabwitsa.+ Mpingo wa oyera anu udzatamanda kukhulupirika kwanu.   Pakuti ndani kumwamba angayerekezeredwe ndi Yehova?+ Ndani angafanane ndi Yehova pakati pa ana a Mulungu?+   Mulungu ayenera kuopedwa pakati pa gulu lake la oyera.+ Iye ndi wamkulu ndi wochititsa mantha kuposa onse omuzungulira.+   Inu Yehova Mulungu wa makamu,+ Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+ Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+   Nyanja ikadzaza mumailamulira.+ Mafunde ake akamawinduka, inuyo mumawakhalitsa bata.+ 10  Mwaphwanya Rahabi*+ ndi kumuchititsa kukhala ngati munthu amene waphedwa.+ Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 11  Kumwamba ndi kwanu,+ dziko lapansi nalonso ndi lanu.+ Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu.+ 12  Munapanga kumpoto ndi kum’mwera.+ Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amafuula mokondwera ndi kutamanda dzina lanu.+ 13  Mkono wamphamvu ndi wanu,+ Dzanja lanu ndi lamphamvu,+ Dzanja lanu lamanja ndi lokwezeka.+ 14  Chilungamo ndi chiweruzo ndizo maziko a mpando wanu wachifumu.+ Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zili pamaso panu.+ 15  Odala ndi anthu amene amafuula mosangalala.+ Iwo amayendabe m’kuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova.+ 16  Iwo amakondwera ndi dzina lanu tsiku lonse.+ Chilungamo chanu chimawakweza,+ 17  Pakuti inu ndinu amene mumachititsa mphamvu zawo kukhala zaulemerero.+ Ndipo mwa kukoma mtima kwanu, nyanga* yathu imakwezedwa.+ 18  Pakuti chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,+ Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+ 19  Pa nthawi imeneyo munalankhula ndi okhulupirika anu mwa masomphenya,+ Ndipo munati: “Ndapereka thandizo kwa wamphamvu.+ Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+ 20  Ndapeza Davide mtumiki wanga,+ Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+ 21  Dzanja langa lolimba lidzakhala pa iye.+ Mkono wanga udzamulimbitsa.+ 22  Palibe mdani amene adzamupondereza,+ Ndipo palibe mwana aliyense wa anthu oipa amene adzamusautsa.+ 23  Ndinaphwanya adani ake zidutswazidutswa ndi kuwachotsa pamaso pake,+ Ndipo odana naye kwambiri ndinapitirizabe kuwamenya.+ 24  Kukhulupirika kwanga ndi kukoma mtima kwanga kosatha kuli pa iye,+ Ndipo nyanga yake imakwezedwa m’dzina langa.+ 25  Ndinaika ulamuliro wake panyanja,+ Ndipo ndinam’patsa ulamuliro pamitsinje.+ 26  Iye amafuula kwa ine kuti, ‘Inu ndinu Atate wanga,+ Mulungu wanga+ ndi Thanthwe la chipulumutso changa.’+ 27  Inenso ndidzamuika kukhala mwana woyamba kubadwa,+ Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse a padziko lapansi.+ 28  Ndidzamusonyeza kukoma mtima kwanga kosatha mpaka kalekale,+ Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+ 29  Ndidzakhazikitsa mbewu yake kwamuyaya,+ Ndipo mpando wake wachifumu udzakhalapo kwa masiku ochuluka ngati masiku a kumwamba.+ 30  Ana ake akadzasiya chilamulo changa,+ Ndi kuleka kutsatira zigamulo zanga,+ 31  Akadzanyoza mfundo zanga, Ndi kusasunga malamulo anga, 32  Ine ndidzawaimba mlandu ndi kuwalanga ndi ndodo,+ Ndipo ndidzawalanga ndi zikoti chifukwa cha zolakwa zawo.+ 33  Koma kukoma mtima kwanga kosatha sindidzakuchotsa pa iye,+ Ndipo sindidzasiya kukhulupirika kwanga.+ 34  Sindidzaphwanya pangano langa,+ Ndipo sindidzasintha mawu otuluka pakamwa panga.+ 35  Ndalumbira kamodzi kokha pa kuyera kwanga,+ Davide sindidzamunamiza.+ 36  Mbewu yake idzakhala mpaka kalekale,+ Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala ngati dzuwa pamaso panga.+ 37  Udzakhazikika ngati mwezi mpaka kalekale, Udzakhala ngati mboni yokhulupirika ya m’mlengalengayo.” [Seʹlah.] 38  Koma inu mwataya wodzozedwa wanu moti mukupitiriza kunyansidwa naye,+ Ndipo mwamukwiyira.+ 39  Mwakana moipidwa pangano la mtumiki wanu. Mwanyoza chisoti chake chachifumu mwa kuchiponyera pansi.+ 40  Mwagwetsa makola ake onse amiyala.+ Mizinda yake yamipanda yolimba mwaisandutsa mabwinja.+ 41  Onse oyenda njira imeneyo afunkha zinthu zake.+ Iye wakhala chinthu chotonzedwa kwa anthu oyandikana naye.+ 42  Mwakweza dzanja lamanja la adani ake.+ Mwachititsa adani ake onse kusangalala.+ 43  Kuwonjezera apo, mukuonanso lupanga lake ngati mdani,+ Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo.+ 44  Mwachititsa kuti kuwala kwake kuthe,+ Mpando wake wachifumu mwauponyera pansi.+ 45  Mwafupikitsa masiku a unyamata wake. Ndipo mwamukulunga ndi manyazi.+ [Seʹlah.] 46  Inu Yehova, kodi mudzadzibisa kufikira liti? Ku nthawi zonse?+ Kodi mkwiyo wanu udzakhalabe ukuyaka ngati moto?+ 47  Kumbukirani utali wa moyo wanga.+ Kodi ana onse a anthu munawalenga pachabe?+ 48  Kodi pali mwamuna wamphamvu aliyense amene sadzaona imfa?+ Kodi angathe kupulumutsa moyo wake m’dzanja la Manda?+ [Seʹlah.] 49  Kodi zochita zanu zakale zija zosonyeza kukoma mtima kosatha zili kuti, inu Yehova? Zija zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+ 50  Inu Yehova, kumbukirani chitonzo chimene chagwera atumiki anu.+ Kumbukirani kuti ndanyamula pachifuwa panga chitonzo cha mitundu yambiri ya anthu.+ 51  Inu Yehova, kumbukirani mmene adani anu alankhulira motonza,+ Mmene atonzera paliponse pamene mapazi a wodzozedwa wanu aponda.+ 52  Adalitsike Yehova mpaka kalekale. Ame! Ame!*+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.
Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo kapena Farao.
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”