Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 88:1-18

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. Kwa wotsogolera nyimbo pa Mahalati.* Iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa m’banja la Zera. 88  Inu Yehova, Mulungu wa chipulumutso changa,+ Masana ndimafuula kwa inu,+ Usikunso ndimafuula pamaso panu.+   Pemphero langa lidzafika kwa inu.+ Tcherani khutu lanu kuti mumve kuchonderera kwanga.+   Pakuti ine ndakumana ndi masoka ochuluka,+ Ndipo moyo wanga wayandikira ku Manda.+   Anandiika m’gulu la anthu otsikira kudzenje.+ Ndakhala ngati mwamuna wanyonga zake koma wopanda mphamvu.+   Ndakhala womasuka ngati anthu akufa,+ Ngati anthu ophedwa amene agona m’manda,+ Anthu amene simukuwakumbukiranso Komanso amene sakulandira thandizo kuchokera m’manja mwanu.+   Mwandiika m’dzenje lakuya kwambiri, M’malo a mdima, m’phompho lalikulu.+   Mkwiyo wanu wagwera pa ine,+ Ndipo mwandisautsa ndi mafunde anu onse amphamvu.+ [Seʹlah.]   Anzanga mwawaika kutali ndi ine.+ Mwandisandutsa chinthu chonyansa kwa iwo.+ Ndatsekerezedwa ndipo sindingathenso kuchoka.+   Diso langa lafooka chifukwa cha kusautsika kwanga.+ Ndaitana inu Yehova tsiku lonse.+ Ndapemphera kwa inu nditakweza manja anga.+ 10  Kodi anthu akufa mudzawachitira zodabwitsa?+ Kapena kodi anthu akufa, anthu amene sangachite kanthu, adzauka?+ Kodi adzakutamandani?+ [Seʹlah.] 11  Kodi adzalengeza za kukoma mtima kwanu kosatha m’manda? Kodi adzalengeza za kukhulupirika kwanu m’malo a chiwonongeko?+ 12  Kodi zodabwitsa zimene inu mukuchita zidzadziwika mu mdima?+ Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika m’dziko la anthu oiwalika?+ 13  Koma ine ndafuulira inu Yehova kupempha thandizo,+ Ndipo m’mawa mapemphero anga amafika kwa inu nthawi zonse.+ 14  Inu Yehova, n’chifukwa chiyani mukunditaya?+ N’chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+ 15  Kuyambira pa unyamata wanga ndakhala ndikusautsika komanso kutsala pang’ono kufa.+ Ndapirira kwambiri zinthu zoopsa zochokera kwa inu.+ 16  Mafunde a mkwiyo wanu woyaka moto andimiza.+ Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandisowetsa chonena.+ 17  Zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.+ Zandimiza pa nthawi imodzi. 18  Bwenzi langa ndi mnzanga mwawaika kutali kwambiri.+ Malo a mdima ndiwo anzanga apamtima.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 53:Kamutu.
Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.