Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 87:1-7

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 87  Maziko a mzinda wa Mulungu ali m’mapiri opatulika.+   Yehova amakonda kwambiri zipata za Ziyoni+ Kusiyana ndi mahema onse a Yakobo.+   Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ [Seʹlah.]   Ine ndidzatchula Rahabi*+ ndi Babulo+ monga ena mwa amene akundidziwa. Ponena za Filisitiya,+ Turo ndi Kusi ine ndidzati: “Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+   Ponena za Ziyoni anthu adzati: “Aliyense anabadwira mmenemo.”+ Ndipo Wam’mwambamwamba+ adzakhazikitsa mzinda umenewo.+   Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:+ “Amenewa anabadwira m’Ziyoni.”+ [Seʹlah.]   Kudzakhalanso oimba komanso ovina gule wovina mozungulira amene adzati:+ “Akasupe anga onse ali mwa iwe.”+

Mawu a M'munsi

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.