Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 86:1-17

Pemphero la Davide. 86  Tcherani khutu inu Yehova. Ndiyankheni,+ Pakuti ndasautsika ndipo ndasauka.+   Tetezani moyo wanga pakuti ndine wokhulupirika.+ Inu ndinu Mulungu wanga, pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani.+   Ndikomereni mtima inu Yehova,+ Pakuti ndimaitana inu tsiku lonse.+   Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu,+ Pakuti ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.+   Pakuti inu Yehova ndinu Mulungu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+ Kukoma mtima kosatha kumene mumawasonyeza onse oitana pa inu ndi kwakukulu.+   Inu Yehova, tcherani khutu ku pemphero langa.+ Ndipo mvetserani mawu a kuchonderera kwanga.+   Pa tsiku la nsautso yanga ndidzaitana pa inu,+ Ndipo inu mudzandiyankha.+   Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu.+ Ndipo palibe ntchito zilizonse zofanana ndi ntchito zanu.+   Mitundu yonse imene munapanga idzabwera kwa inu,+ Ndipo idzagwada pamaso panu, inu Yehova,+ Ndi kulemekeza dzina lanu.+ 10  Pakuti inu ndinu wamkulu ndipo mukuchita zinthu zodabwitsa.+ Inu nokha ndinu Mulungu.+ 11  Inu Yehova, ndilangizeni za njira yanu.+ Ndidzayenda m’choonadi chanu.+ Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.+ 12  Ndikukutamandani inu Yehova Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse,+ Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale, 13  Pakuti kukoma mtima kosatha kumene mwandisonyeza ndi kwakukulu,+ Ndipo mwapulumutsa moyo wanga ku Manda, kumalo apansi penipeni.+ 14  Inu Mulungu, anthu odzitukumula andiukira.+ Khamu la anthu opondereza anzawo likufunafuna moyo wanga,+ Ndipo sanakuikeni patsogolo pawo.+ 15  Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo ndi wachisomo,+ Wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi choonadi.+ 16  Ndicheukireni ndi kundikomera mtima.+ Patsani mtumiki wanu mphamvu,+ Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.+ 17  Ikani chizindikiro cha ubwino wanu pa ine, Kuti anthu odana nane aone zimenezi ndi kuchita manyazi,+ Pakuti inu Yehova mwandithandiza ndi kundilimbikitsa.+

Mawu a M'munsi