Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 85:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 85  Inu Yehova, mwasangalala ndi dziko lanu.+ Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina.+   Mwakhululukira anthu anu zolakwa zawo.+ Mwaphimba machimo awo onse.+ [Seʹlah.]   Mwalamulira mkwiyo wanu wonse,+ Ndipo simunasonyeze kutentha kwa mkwiyo wanu.+   Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale, inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+ Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+   Kodi mupitiriza kutikwiyira mpaka kalekale?+ Kodi mudzasonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?+   Kodi simutitsitsimutsanso+ Kuti anthu anu akondwere chifukwa cha inu?+   Inu Yehova, tisonyezeni kukoma mtima kwanu kosatha,+ Ndipo tipatseni chipulumutso chanu.+   Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanena,+ Pakuti adzanena za mtendere kwa anthu ake+ ndi kwa okhulupirika ake. Koma iwo asadzidalire kwambiri ngati kale.+   Ndithudi, chipulumutso chake chili pafupi ndi amene amamuopa,+ Kuti ulemerero ukhale m’dziko lathu.+ 10  Kukoma mtima kosatha ndi choonadi zakumana.+ Chilungamo ndi mtendere zapsompsonana.+ 11  Choonadi chidzaphuka padziko lapansi,+ Ndipo chilungamo chidzayang’ana pansi kuchokera kumwamba.+ 12  Yehova nayenso adzapereka zinthu zabwino,+ Ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake.+ 13  Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+ Ndipo chidzapanga njira yotsatira mapazi a Mulungu.+

Mawu a M'munsi