Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 84:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora. 84  Inu Yehova wa makamu,+ Ine ndimakondadi chihema chanu chachikulu!+   Ndimalakalaka mabwalo a Yehova ndipo ndafookeratu chifukwa cholakalaka mabwalowo.+ Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.+   Inu Yehova wa makamu, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga, Ngakhale mbalame zapeza malo okhala pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu. Namzeze* wadzimangira chisa chake pamenepo, Ndi kuikamo ana ake!   Odala ndi anthu amene akukhala m’nyumba yanu!+ Iwo akupitirizabe kukutamandani.+ [Seʹlah.]   Odala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+ Amene mtima wawo umalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.+   Poyenda m’chigwa chouma mmene muli zitsamba za baka,*+ Amasandutsa chigwacho kukhala choyenda madzi ochokera pakasupe, Mlangizi wafunda mawu otamanda.+   Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+ Aliyense wa iwo amaonekera kwa Mulungu mu Ziyoni.+   Yehova Mulungu wa makamu, imvani pemphero langa,+ Tcherani khutu, inu Mulungu wa Yakobo.+ [Seʹlah.]   Inu Mulungu chishango chathu, onani,+ Ndipo yang’anani nkhope ya wodzozedwa wanu.+ 10  Pakuti kukhala tsiku limodzi m’mabwalo anu n’kwabwino kuposa kukhala masiku 1,000 kwina.+ Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga+ Kuposa kukhala m’mahema a anthu oipa.+ 11  Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+ Iye amatikomera mtima ndi kutipatsa ulemerero.+ Yehova samana anthu oyenda mosalakwa chinthu chilichonse chabwino.+ 12  Inu Yehova wa makamu, wodala ndi munthu amene amakhulupirira inu.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 8:Kamutu.
Mbalame imeneyi ena amati “kaluweluwe” kapena “kamembe.”
Dzina lakuti “baka” ndi lochokera ku Chiheberi. Chitsamba chimenechi sichikudziwika kuti chinali chotani.