Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 83:1-18

Nyimbo ndi Salimo la Asafu. 83  Inu Mulungu, musakhale chete.+Musakhale phee osalankhulapo kanthu ndipo musakhale duu osachitapo kanthu, inu Mulungu.+   Taonani! Adani anu akuchita phokoso.Anthu odana nanu kwambiri atukula mitu yawo.   Iwo amakumana mwachinsinsi kuti akambirane zochitira chiwembu anthu anu.+Ndipo amakonzera chiwembu anthu anu obisika.+   Iwo anena kuti: “Bwerani tiwafafanize kuti asakhalenso mtundu,Ndi kuti dzina la Isiraeli lisakumbukikenso.”+   Pakuti ndi mtima wonse, iwo amagawana nzeru,+Ndipo anapangana pangano lotsutsana ndi inu.   Amenewa ndi anthu okhala m’mahema a Edomu ndi m’mahema a Isimaeli, Amowabu ndi Ahagara,   Agebala, Aamoni, Aamaleki,Afilisiti pamodzi ndi anthu a ku Turo.+   Asuri nawonso agwirizana nawo,Ndipo amapereka thandizo kwa ana aamuna a Loti. [Seʹlah.]   Muwachitire zimene munachitira Midiyani ndi Sisera.Muwachitirenso zimene munachitira Yabini kuchigwa cha Kisoni. 10  Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.Anasanduka manyowa a m’nthaka. 11  Atsogoleri awo muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.Ndipo mafumu awo onse muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna. 12  Iwo anena kuti: “Tiyeni tilande malo amene Mulungu amakhalako kuti akhale athu.” 13  Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+Ngati mapesi otengeka ndi mphepo.+ 14  Mofanana ndi moto wotentha nkhalango,+Ndiponso malawi a moto woyaka m’mapiri, 15  Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+Ndipo muwasokoneze ndi mphepo yanu yamkuntho.+ 16  Achititseni manyazi,+Kuti anthu afunefune dzina lanu, inu Yehova.+ 17  Achite manyazi ndi kusokonezeka nthawi zonse.+Athedwe nzeru ndi kutheratu,+ 18  Kuti anthu adziwe+ kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,Inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba,+ wolamulira dziko lonse lapansi.+

Mawu a M'munsi