Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 82:1-8

Nyimbo ya Asafu. 82  Mulungu waima pakati pa msonkhano wake,+ Ndipo akuweruza pakati pa milungu kuti:+   “Kodi mudzaweruza mopanda chilungamo,+ Ndi kukondera anthu oipa kufikira liti?+ [Seʹlah.]   Chitirani chilungamo anthu onyozeka ndi ana amasiye.*+ Chitirani chilungamo anthu osautsika ndi osauka.+   Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.+ Alanditseni m’manja mwa anthu oipa.”+   Milunguyo siikudziwa kanthu ndipo siikuzindikira.+ Ikuyendayenda mu mdima,+ Ndipo maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+   “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,+ Ndipo nonsenu ndinu ana a Wam’mwambamwamba.+   Ndithudi, mudzafa mmene anthu onse amafera.+ Ndipo mudzagwa mmene kalonga aliyense amagwera!’”+   Nyamukani inu Mulungu, weruzani dziko lapansi.+ Pakuti inu nokha muyenera kutenga mitundu yonse kukhala yanu.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”