Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 81:1-16

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Salimo la Asafu. 81  Anthu inu, fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu,+ Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.+   Yambani kuimba nyimbo+ ndipo tengani maseche,+ Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.+   Pa tsiku lokhala mwezi, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Pa tsiku looneka mwezi wathunthu, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, loimba pa tsiku la chikondwerero.+   Pakuti limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,+ Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.   Anaika chigamulocho monga chikumbutso kwa Yosefe,+ Pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+ Ndinali kumva chilankhulo chimene sindinali kuchidziwa.+   Mulungu akuti: “Ndinachotsa goli paphewa lake.+ Manja ake anamasuka ndipo sananyamule dengu.+   Pa nthawi ya nsautso unaitana ndipo ine ndinakupulumutsa.+ Ndinayamba kukuyankha m’malo obisika a bingu.+ Ndinakusanthula pamadzi a Meriba.+ [Seʹlah.]   Imvani anthu anga, ndipo ndidzakulangizani ndi kukuchenjezani.+ Zikanakhala bwino ngati mukanandimvera, inu Aisiraeli.+   Pakati panu sipadzakhala mulungu wosadziwika.+ Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+ 10  Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,+ Amene ndinakutulutsani m’dziko la Iguputo.+ Tsegulani pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+ 11  Koma anthu anga sanamvere mawu anga.+ Ndipo Isiraeli sanasonyeze kuti ndi wofunitsitsa kundimvera.+ 12  Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuumitsa mtima wawo.+ Iwo anapitiriza kuyenda mu nzeru zawo.+ 13  Haa! Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+ Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda m’njira zanga.+ 14  Ndikanagonjetsa adani awo mosavuta,+ Ndipo ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+ 15  Koma odana kwambiri ndi Yehova adzabwera kwa iye akunjenjemera ndi mantha,+ Ndipo nthawi yawo idzakhala mpaka kalekale. 16  Ine ndidzadyetsa Aisiraeli tirigu wabwino koposa,+ Ndipo ndidzawapatsa  uchi wochokera pathanthwe+ kuti adye ndi kukhuta.”

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 8:Kamutu.