Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 80:1-19

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Chikumbutso.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 80  Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+ Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+ Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+   Sonyezani mphamvu zanu pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase,+ Ndipo bwerani mudzatipulumutse.+   Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+ Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+   Inu Yehova Mulungu wa makamu, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?+   Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,+ Ndipo mukuwamwetsabe misozi yochuluka kwambiri.+   Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azimenyana polimbirana ifeyo.+ Ndipo adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+   Inu Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+ Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+   Munachititsa mtengo wa mpesa kuchoka mu Iguputo.+ Munapitikitsa mitundu ya anthu kuti mubzalemo mtengowo.+   Munalambula malo obzalapo mtengo wa mpesawo+ kuti uzike mizu ndi kudzaza dziko.+ 10  Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake, Ndipo mikungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.+ 11  Pang’onopang’ono nthambi zake zinafika kunyanja,+ Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.*+ 12  N’chifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wake wamiyala?+ Ndipo n’chifukwa chiyani anthu onse odutsa mumsewu akuthyola zipatso zake?+ 13  Nguluwe ikuwononga mtengowo,+ Ndipo magulu a nyama zakutchire akuudya.+ 14  Inu Mulungu wa makamu, chonde bwererani.+ Yang’anani pansi pano muli kumwambako, ndipo onani ndi kusamalira mtengo wa mpesa uwu.+ 15  Onani muzu umene dzanja lanu lamanja linabzala.+ Muonenso mwana wanu amene munamulimbitsa kuti inu mulemekezeke.+ 16  Watenthedwa ndi moto ndi kudulidwa.+ Iwo amawonongeka ndi kudzudzula kwa pankhope panu.+ 17  Dzanja lanu likhale pa munthu wa kudzanja lanu lamanja,+ Ndipo likhale pa mwana wa munthu amene mwamulimbitsa kuti mulemekezeke.+ 18  Ndipo ife sitidzabwerera kukusiyani.+ Tisungeni amoyo kuti tiitane pa dzina lanu.+ 19  Inu Yehova Mulungu wa makamu, tibwezeretseni mwakale.+ Walitsani nkhope yanu kuti tipulumutsidwe.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 45:Kamutu.
Onani Sl 60:Kamutu.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.