Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 8:1-9

Kwa wotsogolera nyimbo pa Gititi.*+ Nyimbo ya Davide. 8  Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,+ Inuyo ulemerero wanu ukusimbidwa kumwambamwamba!+   M’kamwa mwa ana aang’ono ndi ana oyamwa mwakhazikitsamo zamphamvu,+ Chifukwa cha amene akukuchitirani zoipa.+ Mwatero kuti mugonjetse mdani wanu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa.+   Ndikayang’ana kumwamba, ntchito ya zala zanu,+ Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+   Ndimaganiza kuti: Munthu+ ndani kuti muzimuganizira,+ Ndipo mwana wa munthu wochokera kufumbi ndani kuti muzimusamalira?+   Munamuchepetsa pang’ono poyerekeza ndi ena onga Mulungu,*+ Kenako munamuveka ulemerero+ ndi ulemu monga chisoti chachifumu.+   Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+ Mwaika zonse pansi pa mapazi ake:+   Nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe zamphongo, zonse zimenezi,+ Komanso zilombo zakutchire.+   Mbalame zam’mlengalenga ndi nsomba za m’nyanja,+ Chilichonse choyenda m’njira za pansi pa nyanja.+   Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!+

Mawu a M'munsi

“Gititi” ndi mawu achiheberi amene anali kuwagwiritsa ntchito polemba nyimbo, koma tanthauzo lake lenileni silikudziwika.
Kapena kuti “angelo.”