Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 79:1-13

Nyimbo ya Asafu. 79  Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa m’dziko limene ndilo cholowa chanu.+ Aipitsa kachisi wanu woyera.+ Awononga Yerusalemu ndi kumusandutsa bwinja.+   Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo.+ Matupi a okhulupirika anu awapereka kwa zilombo zakutchire.+   Atsanula magazi awo ngati madzi Kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wowaika m’manda.+   Anthu oyandikana nafe akutitonza,+ Anthu otizungulira akutinyoza ndi kutiseka.+   Haa! Inu Yehova, mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+ Kodi mkwiyo wanu udzakhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+   Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+ Ndi pa maufumu amene sakuitana pa dzina lanu.+   Pakuti iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo,+ Ndipo malo ake okhalamo awasandutsa bwinja.+   Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+ Fulumirani! Tisonyezeni chifundo chanu,+ Chifukwa tasautsika koopsa.+   Tithandizeni inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+ Kuti dzina lanu lilemekezedwe.+ Tipulumutseni ndi kutikhululukira* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+ 10  Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+ Pamene mukubwezera anthu a mitundu inawo chifukwa cha magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa,+ Ife tidzaone ndi maso athu.+ 11  Mverani kuusa moyo kwa mkaidi.+ Anthu opita kukaphedwa muwateteze ndi dzanja lanu lamphamvu.+ 12  Bwezerani anthu oyandikana nafe mwa kuwatsanulira chitonzo pachifuwa pawo maulendo 7,+ Inu Yehova, muwabwezere chitonzo chimene anachita pa inu.+ 13  Koma ife, anthu anu, nkhosa zimene mukuweta,+ Tidzakuyamikani mpaka kalekale. Tidzakutamandani ku mibadwomibadwo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “kuphimba.”