Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 78:1-72

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 78  Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.+Tcherani khutu ku mawu a pakamwa panga.+   Ndidzatsegula pakamwa panga ndi kunena mwambi.+Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale,+   Amene tinamva ndipo tikuwadziwa,+Komanso amene makolo athu anatifotokozera.   Mbadwa zawo sitikuzibisira mawu ophiphiritsawa,Ndipo tidzawasimba ngakhale ku mibadwo ya m’tsogolo.Tidzasimba ntchito zotamandika za Yehova ndi mphamvu zake,+Komanso zinthu zodabwitsa zimene wachita.+   Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,Iye anaika chilamulo mu Isiraeli,Zinthu zimene analamula makolo athu,+Kuti auze ana awo.   Kuti m’badwo wa m’tsogolo, ana amene adzabadwe m’tsogolo, adzadziwe zimenezi,+Kuti nawonso adzanyamuke ndi kusimbira ana awo.   Kuti anawo azidzadalira Mulungu,+Ndi kuti asadzaiwale zochita za Mulungu koma kuti azidzasunga malamulo ake.   Ndipo asadzakhale ngati makolo awo,M’badwo wosamva ndi wopanduka,M’badwo umene sunakonze mtima wawo,Ndipo maganizo awo sanali okhulupirika kwa Mulungu.   Ana a Efuraimu, ngakhale kuti anali ndi mivi ndi mauta,Anathawa pa tsiku lankhondo. 10  Iwo sanasunge pangano la Mulungu,Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake. 11  Iwo anayambanso kuiwala zochita zake,Ndi ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+ 12  Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awoM’dziko la Iguputo,+ m’dera la Zowani. 13  Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,Ndipo anaimitsa madzi kukhala ngati khoma. 14  Iye anapitiriza kuwatsogolera ndi mtambo masana,Ndipo usiku wonse anali kuwatsogolera ndi kuwala kwa moto. 15  Iye anang’amba miyala m’chipululuKuti awapatse madzi akumwa ochuluka ngati a m’nyanja.+ 16  Iye anatulutsa madzi ambiri pathanthwe,Ndipo anachititsa madzi kutsika ngati mitsinje.+ 17  Koma iwo anapitiriza kumuchimwiraMwa kupandukira Wam’mwambamwamba m’dera lopanda madzi. 18  Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu m’mitima yawo+Mwa kupempha chakudya china chimene mtima wawo unalakalaka. 19  Pamenepo anayamba kulankhula mawu oipa kwa Mulungu.Iwo anati: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya m’chipululu muno?” 20  Taonani! Kodi Mulungu si uja anamenya thanthweKuti madzi atuluke, kutinso patuluke mitsinje yodzaza madzi?Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,Kapena kodi angakonzere anthu ake chakudya?” 21  Choncho Yehova anamva zimenezo ndipo anakwiya.Moti moto unayakira Yakobo,Ndipo mkwiyo unatsikira pa Isiraeli. 22  Pakuti iwo sanakhulupirire Mulungu.+Sanakhulupirire kuti iye adzawapulumutsa. 23  Pamenepo Mulungu analamula mitambo ya m’mlengalenga,Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba. 24  Ndipo anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.Iye anawapatsa tirigu wochokera kumwamba. 25  Anthu anadya chakudya cha amphamvu.+Iye anawatumizira chakudya chokwanira. 26  Anachititsa mphepo ya kum’mawa kuwomba m’mlengalenga,Ndipo mwa mphamvu zake anachititsa mphepo ya kum’mwera kuwomba.+ 27  Iye anagwetsa chakudya pa iwo ngati fumbi.Anawagwetsera zolengedwa zamapiko zouluka, zochuluka ngati mchenga wakunyanja. 28  Anapitiriza kuwagwetsera zimenezi mumsasa wake,Kuzungulira mahema ake onse. 29  Iwo anadya ndi kukhuta kwambiri.+Iye anawabweretsera zimene anali kulakalaka. 30  Iwo anafunabe chakudya china,Pamene china chinali m’kamwa. 31  Nthawi yomweyo, mkwiyo wa Mulungu unatsikira pa iwo.Iye anayamba kupha anthu awo amphamvu.Ndipo anakomola anyamata a mu Isiraeli. 32  Ngakhale zinali choncho, iwo anawonjezera machimo awo,Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa. 33  Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya wotuluka m’mphuno.Anadula zaka za moyo wawo ndi masoka. 34  Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo anali kumufunafuna.Anali kutembenuka ndi kuyamba kufunafuna Mulungu. 35  Iwo anali kukumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,Ndiponso kuti Mulungu Wam’mwambamwamba anali Wowabwezerera. 36  Koma iwo anali kufuna kum’pusitsa ndi pakamwa pawo.+Ndi lilime lawo anali kufuna kunena bodza kwa iye.+ 37  Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.Ndipo iwo sanakhulupirike ku pangano lake. 38  Koma anawamvera chifundo. Anali kukhululukira* machimo awo+ ndipo sanali kuwawononga.Nthawi zambiri anali kubweza mkwiyo wake,Ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse. 39  Iye anali kukumbukira nthawi zonse kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+Anali kukumbukira kuti moyo wawo umachoka ndipo subwereranso.+ 40  Iwo analitu kumupandukira kawirikawiri m’chipululu,Anali kumukhumudwitsa m’chipululumo!+ 41  Mobwerezabwereza, anali kumuyesa Mulungu,Ndipo anali kumvetsa chisoni Woyera wa Isiraeli. 42  Iwo sanakumbukire dzanja la Mulungu,Sanakumbukire tsiku limene anawawombola kwa mdani wawo, 43  Iwo sanakumbukire mmene anaikira zizindikiro zake mu Iguputo,Ndi zozizwitsa zimene anachita m’dera la Zowani,+ 44  Mmene anasinthira mitsinje ing’onoing’ono yotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,Moti sanathe kumwa madzi ake.+ 45  Mulungu anawatumizira tizilombo toyamwa magazi kuti tiwadye,Ndi achule kuti awawononge. 46  Anapereka zokolola zawo kwa mphemvu,Ndipo ntchito yawo yolemetsa anaipereka kwa dzombe. 47  Anapha mitengo yawo ya mpesa ndi mvula yamatalala.Anapha mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala.+ 48  Anaphanso nyama zawo zonyamula katundu ndi matalala,Ndiponso ziweto zawo ndi mliri wakupha. 49  Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,+Ukali, ziweruzo zamphamvu ndi masautso.+Anawatumizira makamu a angelo obweretsa masoka. 50  Mkwiyo wake anaulambulira njira.Sanawabweze kuwachotsa ku imfa.Ndipo anawapha ndi mliri. 51  Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa mu Iguputo,Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka m’mahema a Hamu.+ 52  Kenako anachititsa anthu ake kuchoka m’dzikolo ngati gulu la nkhosa,+Anawayendetsa m’chipululu ngati gulu la ziweto.+ 53  Anapitiriza kuwatsogolera ndi kuwateteza ndipo iwo sanachite mantha.Nyanja inamiza adani awo. 54  Kenako anawalowetsa m’dziko lake lopatulika,M’dera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+ 55  Chifukwa cha iwo anachotsa mitundu ina pang’onopang’ono m’dzikoli,Ndipo anayesa dzikoli ndi kuligawa kwa iwo kukhala cholowa chawo,Moti anachititsa mafuko a Isiraeli kukhala m’nyumba zawozawo. 56  Koma iwo anayamba kuyesa Mulungu Wam’mwambamwamba ndi kum’pandukira,Ndipo sanasunge zikumbutso zake. 57  Iwo anali kubwerera ndi kuchita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.Anapotoka maganizo ngati uta wosakunga kwambiri.+ 58  Iwo anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,Ndipo anamuchititsa nsanje ndi zifaniziro zawo zogoba. 59  Mulungu anamva+ ndipo anakwiya kwambiri.Chotero ananyansidwa kwambiri ndi Isiraeli.+ 60  Pamapeto pake anasiya chihema chopatulika cha ku Silo,Hema limene anali kukhalamo pakati pa anthu ochokera kufumbi. 61  Analola kuti chizindikiro cha mphamvu zake chitengedwe ndi adani ake,+Iye analola kuti chizindikiro cha kukongola kwake chikhale m’manja mwa adani. 62  Iye anapereka anthu ake ku lupanga,Ndipo anakwiyira cholowa chake.+ 63  Anyamata ake ananyeka ndi moto,Ndipo anamwali ake sanatamandidwe. 64  Ansembe ake anagwa ndi lupanga,Ndipo akazi awo amasiye sanalire. 65  Pamenepo Yehova anagalamuka ngati akudzuka kutulo,+Ngati munthu wamphamvu amene akugalamuka pambuyo pomwa vinyo wambiri.+ 66  Iye anathamangitsa adani ake ndi kuwapha.+Anawachititsa kuti akhale akutonzedwa mpaka kalekale.+ 67  Iye anakana hema wa Yosefe,+Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu.+ 68  Koma anasankha fuko la Yuda,Phiri la Ziyoni limene analikonda.+ 69  Anayamba kumanga malo opatulika ngati malo okwera a paphiri,Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+ 70  Choncho anasankha Davide mtumiki wake,Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa. 71  Anamutenga kumene anali kuweta nkhosa zoyamwitsa,Anamutenga kuti akhale m’busa wa ana a Yakobo amene ndi anthu ake,Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake. 72  Iye anayamba kuwaweta malinga ndi mtima wake wosagawanika,Ndipo anayamba kuwatsogolera mwaluso.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.
Mawu ake enieni, “kuphimba.”