Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 77:1-20

Kwa wotsogolera nyimbo pa Yedutuni. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 77  Ndidzafuulira Mulungu,+ Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzatchera khutu lake kwa ine.+   Pa tsiku la zowawa zanga ndafunafuna Yehova.+ Ndakweza dzanja langa kumwamba usiku wonse, ndipo silinachite dzanzi. Koma sindinatonthozeke.+   Ndidzakumbukira Mulungu ndipo ndidzavutika maganizo.+ Ine ndasautsika. N’chifukwa chake ndafooka.+ [Seʹlah.]   Mwatsegula zikope zanga,+ Ndipo ndavutika mtima, moti sindingathe kulankhula.+   Ndaganizira za masiku akale,+ Ndaganizira zaka za makedzana.   Usiku ndidzakumbukira nyimbo zanga zoimbidwa ndi chipangizo cha zingwe.+ Ndidzasonyeza kudera nkhawa mumtima mwanga,+ Ndipo ndidzasinkhasinkha zinthu zonse mozama.   Kodi Yehova watitaya mpaka kalekale?+ Kodi sitidzathanso kumusangalatsa?+   Kodi kukoma mtima kwake kosatha wakusiya mpaka muyaya?+ Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa+ ku mibadwomibadwo?   Kodi Mulungu waiwala kukhala wokoma mtima,+ Kapena watsekereza chifundo chake mwaukali?+ [Seʹlah.] 10  Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundisautsa n’zakuti,+ Wam’mwambamwamba wasiya kutipatsa thandizo”?+ 11  Ndidzakumbukira zochita za Ya,+ Ndithu ndidzakumbukira ntchito yanu yodabwitsa yakale.+ 12  Ndidzasinkhasinkha za ntchito zanu zonse,+ Ndipo ndiziganizira zochita zanu.+ 13  Inu Mulungu, njira yanu ili m’malo oyera.+ Kodi ndi Mulungu wamkulu uti amene angafanane ndi Mulungu wathu?+ 14  Inu ndinu Mulungu woona amene mukuchita zodabwitsa.+ Mphamvu zanu mwazidziwikitsa pakati pa mitundu ya anthu.+ 15  Ndi dzanja lanu mwawombola anthu anu,+ Ana aamuna a Yakobo ndi Yosefe. [Seʹlah.] 16  Madzi akuonani, inu Mulungu, Madzi akuonani, ndipo ayamba kumva ululu woopsa.+ Komanso madzi akuya ayamba kuwinduka.+ 17  Mitambo yatulutsa mabingu ndi kugwetsa madzi.+ Thambo latulutsa mkokomo. Mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+ 18  Phokoso la bingu lanu linali ngati la mawilo a galeta.+ Mphezi zinaunika padziko.+ Ndipo dziko lapansi linagwedezeka ndi kuyamba kunjenjemera.+ 19  Msewu wanu unadutsa panyanja,+ Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri. Mmene mapazi anu anaponda simunaoneke. 20  Mwatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+ Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+

Mawu a M'munsi