Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 76:1-12

Kwa wotsogolera nyimbo: Iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 76  Mulungu amadziwika mu Yuda.+ Dzina lake ndi lalikulu mu Isiraeli.+   Malo ake opumulirako ali ku Salemu,+ Malo ake okhalamo ali ku Ziyoni.+   Kumeneko wathyola mivi yoyaka moto,+ Wathyola chishango, lupanga ndi zida zankhondo.+ [Seʹlah.]   Inu Mulungu, mwazunguliridwa ndi kuwala, ndipo ndinu wochititsa nthumanzi kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.+   Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo,+ Iwo awodzera ndi kugona tulo,+ Ndipo palibe ngakhale mmodzi mwa anthu onse olimba mtimawo amene ali ndi mphamvu zotsutsa.+   Hatchi komanso wokwera galeta agona tulo tofa nato chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo.+   Inu ndinu wochititsa mantha,+ Ndani angaime pamaso panu inu mutakwiya kwambiri?+   Munachititsa ziweruzo  zanu kumveka kuchokera kumwambako.+ Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala duu+   Pamene Mulungu ananyamuka ndi kupereka chiweruzo,+ Kuti apulumutse anthu onse ofatsa padziko lapansi.+ [Seʹlah.] 10  Pakuti mkwiyo wa munthu udzakutamandani,+ Mkwiyo wake wotsala mudzaumangirira m’chiuno mwanu. 11  Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+ Bweretsani mphatso mwamantha.+ 12  Mulungu adzatsitsa atsogoleri odzikuza.+ Iye ndi wochititsa mantha kwa mafumu a padziko lapansi.+

Mawu a M'munsi