Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 75:1-10

Kwa wotsogolera nyimbo. “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+ 75  Timakuyamikani, inu  Mulungu, timakuyamikani,+ Ndipo dzina lanu lili pafupi ndi ife.+ Anthu ayenera kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+   Mulungu akuti:* “Ndinasankha nthawi yoikidwiratu,+ Ndipo ndinayamba kuweruza mwachilungamo.+   Dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo anayamba kusungunuka chifukwa cha mantha,+ Ndine amene ndinakonzanso zipilala zake.”+ [Se′lah.]   Anthu opusa ndinawauza kuti: “Musakhale opusa,”+ Ndipo oipa ndinawauza kuti: “Musakweze nyanga.*+   Musakweze nyanga yanu pamwamba. Musalankhule modzikuza.+   Pakuti kukwezeka kwa munthu sikuchokera kum’mawa, Kumadzulo kapena kum’mwera.   Mulungu ndiye woweruza.+ Amatsitsa wina ndi kukweza wina.+   M’dzanja la Yehova muli kapu.+ Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu. Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake. Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+   Koma ine ndidzasimba zimenezi mpaka kalekale. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.+ 10  Mulungu akuti:* “Ndidzadula nyanga zonse za anthu oipa.”+ Koma nyanga za munthu wolungama zidzakwezedwa.+

Mawu a M'munsi

M’Malemba achiheberi mulibe mawu akuti “Mulungu akuti,” koma aikidwapo pofuna kusonyeza amene akulankhula m’mavesi 2 ndi 3.
Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Onani mawu a m’munsi pa vesi 2.