Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 74:1-23

Masikili.* Salimo la Asafu.+ 74  Inu Mulungu, n’chifukwa chiyani mwatitaya?+ N’chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira nkhosa zimene mukuweta?+   Kumbukirani anthu amene munawatenga kukhala anu kalelo,+ Fuko limene munaliwombola monga cholowa chanu,+ Ndi phiri la Ziyoni ili mmene inu mukukhala.+   Pitani kumalo amene awonongedwa.+ M’malo oyera, mdani wachitira zoipa china chilichonse.+   Anthu amene akukuchitirani zoipa afuula mosangalala kuti apambana m’malo anu olambiriramo.+ Aikamo mbendera zawo monga zizindikiro.+   Iwo amatchuka ngati munthu amene amagwetsa mitengo ndi nkhwangwa m’nkhalango.   Ndipo tsopano zojambula mochita kugoba za  m’makoma a malo opatulika, onse amazichotsa ndi nkhwangwa komanso ndodo zokhala ndi chitsulo kumutu kwake.+   Iwo atentha malo anu opatulika.+ Aipitsa ndi kugwetsera pansi chihema chokhala ndi dzina lanu.+   Iwo, ngakhalenso ana awo, onse pamodzi anena mumtima mwawo kuti: “Malo onse olambiriramo a Mulungu ayenera kutenthedwa m’dzikoli.”+   Zizindikiro zathu sitinazione, ndipo palibenso mneneri amene watsala,+ Pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zikhala choncho mpaka liti. 10  Inu Mulungu, kodi mdani adzakuchitirani mopanda ulemu kufikira liti?+ Kodi mdani adzanyoza dzina lanu kwamuyaya?+ 11  N’chifukwa chiyani mwachotsa dzanja lanu, dzanja lanu lamanja,+ Pachifuwa panu koma osachitapo kanthu? Kodi mukatero ife sitiwonongedwa? 12  Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,+ Iye ndiye wondipatsa chipulumutso chachikulu padziko lapansi.+ 13  Inu munavundula nyanja ndi mphamvu zanu.+ Pakati pa madzi munadula mitu ya zilombo za m’nyanja.+ 14  Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani*+ kukhala zidutswazidutswa. Munaipereka kwa anthu monga chakudya, munaipereka kwa anthu okhala m’madera opanda madzi.+ 15  Ndinu amene munang’amba nthaka ndi kupanga akasupe ndi makwawa.+ Inu munaumitsa mitsinje imene inali kukhala ndi madzi nthawi zonse.+ 16  Usana ndi wanu, usikunso ndi wanu.+ Inu munapanga chounikira, munapanga dzuwa.+ 17  Ndinu amene munaika malire onse a dziko lapansi.+ Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+ 18  Kumbukirani izi: Inu Yehova, mdani wakuchitirani mopanda ulemu,+ Ndipo anthu opusa anyoza dzina lanu.+ 19  Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa chilombo chakuthengo.+ Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu osautsika.+ 20  Kumbukirani pangano limene munachita nafe,+ Pakuti malo a mdima a dziko lapansi adzaza ndi chiwawa.+ 21  Musalole kuti munthu woponderezedwa achite manyazi.+ Munthu wosautsika ndi wosauka atamande dzina lanu.+ 22  Nyamukani inu Mulungu, weruzani mlandu wanu.+ Kumbukirani mmene munthu wopusa wakunyozerani tsiku lonse.+ 23  Musaiwale mawu a anthu amene akukuchitirani zoipa.+ Phokoso la anthu okuukirani likukwera kumwamba nthawi zonse.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 32:Kamutu.
Kapena kuti “ng’ona.”