Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 73:1-28

Nyimbo ya Asafu.+ 73  Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+   Koma ine phazi langa linangotsala pang’ono kupatuka,+ Mapazi anga anangotsala pang’ono kuterereka.+   Pakuti ndinachitira nsanje anthu odzitukumula,+ Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+   Pakuti samva zowawa za imfa.+ Ndipo mimba zawo ndi zazikulu chifukwa cha kunenepa.+   Iwo sakumana ndi mavuto amene anthu onse amakumana nawo,+ Ndipo sakumana ndi masoka mofanana ndi anthu ena onse.+   Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda m’khosi mwawo,+ Ndipo avala chiwawa ngati malaya.+   Diso lawo latuzuka chifukwa cha kunenepa.+ Achita zambiri kuposa zolingalira za mtima wawo.+   Iwo amanyodola ndi kulankhula zinthu zoipa.+ Amalankhula za chinyengo chawo modzikweza.+   Kudzikweza kwawo kwafika kumwamba,+ Akuyendayenda padziko lapansi ndipo lilime lawo likunena zilizonse zimene akufuna.+ 10  Choncho woipa amatengera anthu a Mulungu kumalo omwewo, Ndipo amamwa madzi m’kapu yodzaza bwino. 11  Iwo anena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+ Kodi Wam’mwambamwamba akudziwa zimenezi?”+ 12  Onani! Awa ndi anthu oipa, amene akukhala mosatekeseka mpaka kalekale.+ Iwo achulukitsa chuma chawo.+ 13  Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,+ Ndipo ndasamba m’manja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wopanda cholakwa.+ 14  Ndinali kukumana ndi masoka tsiku lililonse,+ Ndipo m’mawa uliwonse ndinali kudzudzulidwa.+ 15  Ngati ndikananena kuti: “Ndidzalankhula za zinthu zimenezi,” Pamenepo ndikanachitira chinyengo M’badwo wa ana anu aamuna.+ 16  Ndipo ndinali kuganizira nkhani imeneyi kuti ndiimvetse.+ Zinali zopweteka kwa ine, 17  Kufikira pamene ndinalowa m’malo opatulika aulemerero a Mulungu.+ Ndinafuna kudziwa za tsogolo lawo.+ 18  Ndithudi, mwawaimika pamalo oterera.+ Mwawagwetsa kuti awonongeke.+ 19  Haa! M’kanthawi kochepa, iwo akhala chinthu chodabwitsa.+ Afika pamapeto awo ndipo atha chifukwa cha masoka owagwera modzidzimutsa! 20  Inu Yehova, anthu amenewa ali ngati maloto amene aiwalika podzuka.+ Choncho pamene mukuimirira mudzawakana mochititsa manyazi.+ 21  Pakuti mtima unandipweteka+ Ndipo ndinamva ululu mu impso zanga.+ 22  Ndinakhala wopanda nzeru ndipo sindinadziwe kanthu.+ Ndinakhala ngati nyama yakuthengo pamaso panu.+ 23  Koma ine ndili ndi inu nthawi zonse.+ Mwandigwira dzanja langa lamanja.+ 24  Mudzanditsogolera ndi malangizo anu,+ Ndipo pambuyo pake mudzanditenga ndi kundipatsa ulemerero.+ 25  Winanso ndani kumwambako amene ali kumbali yanga?+ Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha.+ 26  Thupi langa ndi mtima wanga zalefuka.+ Mulungu ndiye thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+ 27  Pakuti onse okhala kutali ndi inu adzatheratu.+ Mudzawononga ndithu aliyense wochita chigololo mwa kukusiyani.+ 28  Koma kwa ine kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawirapo panga,+ Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Mawu a M'munsi