Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 72:1-20

Salimo lonena za Solomo. 72  Inu Mulungu, dziwitsani mfumu za zigamulo zanu,+ Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+   Aweruzire anthu milandu mwachilungamo,+ Ndipo aweruze milandu ya osautsika ndi ziweruzo zolungama.+   Mapiri atenge mtendere ndi kupita nawo kwa anthu,+ Komanso zitunda zitenge mtendere wopezeka mwachilungamo.   Aweruze osautsika pakati pa anthu,+ Apulumutse ana a anthu osauka, Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.   Iwo adzakuopani nthawi zonse pamene dzuwa likuwala,+ Adzakuopani ku mibadwomibadwo pamene mwezi uli kuthambo.+   Adzatsika ngati mvula pa udzu umene wadulidwa,+ Ngati mvula yambiri yamvumbi imene imanyowetsa kwambiri nthaka.+   M’masiku ake, wolungama adzaphuka,+ Ndipo padzakhala mtendere wochuluka kwa nthawi yonse pamene mwezi udzakhalepo.+   Ndipo adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,+ Komanso kuchokera ku Mtsinje*+ kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+   Anthu okhala m’madera opanda madzi adzagwada pamaso pake,+ Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+ 10  Mafumu a ku Tarisi ndi m’zilumba+ Adzapereka msonkho.+ Mafumu a ku Sheba ndi Seba Adzapereka mphatso.+ 11  Mafumu onse adzamugwadira ndi kumuweramira.+ Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.+ 12  Pakuti adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,+ Komanso wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza.+ 13  Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,+ Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.+ 14  Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa, Ndipo adzaona magazi awo kukhala amtengo wapatali.+ 15  Iye akhale ndi moyo wautali,+ ndipo apatsidwe wina mwa golide wa ku Sheba.+ Nthawi zonse anthu azimupempherera. Adalitsike tsiku lililonse.+ 16  Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+ Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.+ Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+ Ndipo anthu ochokera mumzinda adzaphuka ngati udzu wa panthaka.+ 17  Dzina lake likhalebe mpaka kalekale.+ Nthawi zonse pamene dzuwa latuluka, dzina lake lizitchuka, Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.*+ Mitundu yonse ya anthu imutche wodala.+ 18  Adalitsike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+ Iye yekha amene akuchita ntchito zodabwitsa.+ 19  Lidalitsike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+ Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+ Ame! Ame!* 20  Mapemphero a Davide mwana wa Jese,+ athera pamenepa.

Mawu a M'munsi

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti “adzadzidalitsa okha,” kusonyeza kuti akufunika kuchitapo kanthu kuti alandire madalitso amenewo.
Kapena kuti “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”