Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 71:1-24

71  Inu Yehova, ine ndathawira kwa inu.+ Musalole kuti ndichite manyazi.+   Mundilanditse chifukwa  cha chilungamo chanu ndipo mundipulumutse.+ Tcherani khutu lanu kwa ine ndi kundipulumutsa.+   Mukhale thanthwe lachitetezo loti ndizilowamo nthawi zonse.+ Lamulani kuti ndipulumutsidwe,+ Pakuti inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+   Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni m’manja mwa woipa,+ Ndipulumutseni m’manja mwa munthu wochita zinthu mopanda chilungamo komanso mopondereza.+   Pakuti chiyembekezo changa ndinu,+ Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, ndimadalira inu kuyambira pa unyamata wanga.+   Kuyambira ndili m’mimba mwa mayi anga inu mwandithandiza.+ Inu ndi amene munanditulutsa m’mimba mwa mayi anga.+ Ndimatamanda inu nthawi zonse.+   Ndakhala ngati chozizwitsa kwa anthu ambiri,+ Koma inu ndinu malo anga olimba othawirako.+   M’kamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu,+ Ndipo pakamwa panga pakunena za ulemerero wanu tsiku lonse.+   Musanditaye nthawi ya ukalamba wanga.+ Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zikutha.+ 10  Pakuti adani anga anena za ine,+ Ndipo anthu olondalonda moyo wanga, onse pamodzi achita upo,+ 11  Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya.+ Mulondoleni ndi kumugwira pakuti palibe womulanditsa.”+ 12  Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.+ Inu Mulungu wanga, fulumirani kundithandiza.+ 13  Anthu otsutsana nane achite manyazi, iwo awonongedwe.+ Amene akufunafuna kundigwetsera tsoka adziphimbe ndi chitonzo ndiponso manyazi.+ 14  Koma ine ndidzayembekezera inu nthawi zonse,+ Ndipo ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale. 15  Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+ Padzanena za chipulumutso chanu tsiku lonse,+ Pakuti ntchito za chilungamo ndi chipulumutso chanu ndi zochuluka ndipo sindinathe kuziwerenga.+ 16  Ndidzabwera ndi kunena za mphamvu zanu zazikulu,+ inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.+ Ndidzanena za chilungamo chanu, osati cha wina aliyense.+ 17  Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira pa unyamata wanga,+ Ndipo mpaka pano ndikunena za ntchito zanu zodabwitsa.+ 18  Ngakhale nditakalamba ndi kumera imvi, inu Mulungu musandisiye,+ Kufikira nditanena za dzanja lanu lamphamvu ku m’badwo wotsatira,+ Kufikira nditanena za mphamvu zanu kwa onse obwera m’tsogolo.+ 19  Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+ Tikanena za zinthu zazikulu zimene munachita,+ Inu Mulungu, ndani angafanane ndi inu?+ 20  Chifukwa chakuti mwandionetsa masautso ndi masoka ambiri,+ Nditsitsimutseni.+ Nditulutseninso m’madzi akuya, pansi pa nthaka.+ 21  Kulitsani ulemu wanga,+ Mundizungulire ndi chitetezo chanu ndi kundilimbikitsa.+ 22  Inenso ndidzakutamandani ndi chipangizo cha zingwe,+ Ndidzatamanda choonadi chanu, inu Mulungu.+ Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi zeze, Inu Woyera wa Isiraeli.+ 23  Ndikafuna kuimba nyimbo zokutamandani, pakamwa panga padzafuula mokondwera,+ Ngakhalenso moyo wanga umene mwauwombola+ udzakutamandani. 24  Ngakhalenso lilime langa lidzalankhula chapansipansi za chilungamo chanu tsiku lonse,+ Pakuti ofunafuna kundigwetsera tsoka achita manyazi ndipo athedwa nzeru.+

Mawu a M'munsi