Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 70:1-5

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.+ 70  Inu Mulungu, fulumirani kundilanditsa,+ Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+   Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+ Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+   Amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!” abwerere chifukwa cha manyazi awo.+   Onse amene akufunafuna inu akondwere ndi kusangalala mwa inu,+ Ndipo onse amene amakonda chipulumutso chanu, nthawi zonse azinena kuti: “Mulungu alemekezeke!”+   Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+ Inu Mulungu, chitanipo kanthu mwamsanga kuti zinthu zindiyendere bwino.+ Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+ Inu Yehova musachedwe.+

Mawu a M'munsi