Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 69:1-36

Kwa wotsogolera nyimbo pa Maluwa.*+ Salimo la Davide. 69  Ndipulumutseni, inu Mulungu, pakuti madzi afika m’khosi.+   Ndamila m’matope akuya, mmene mulibe malo oponda.+ Ndalowa m’madzi akuya, Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+   Ndatopa ndi kufuula kwanga,+ Mawu asasa pammero panga. Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+   Anthu amene amadana nane popanda chifukwa achuluka kuposa tsitsi la m’mutu mwanga.+ Amene akufuna kunditsitsira kuli chete, chifukwa chodana nane popanda chifukwa, achuluka kwambiri.+ Ngakhale kuti sindine wakuba, anandikakamiza kubweza zinthu zimene zinabedwa.   Inu Mulungu, mwadziwa kupusa kwanga, Ndipo kupalamula kwanga sikunabisike kwa inu.+   Onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,+ Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa makamu.+ Onse amene akufunafuna inu, asanyazitsidwe chifukwa cha ine,+ Inu Mulungu wa Isiraeli.+   Ine ndanyamula chitonzo chifukwa cha inu,+ Manyazi aphimba nkhope yanga.+   Ndadzipatula pakati pa abale anga,+ Ndipo ndakhala mlendo pakati pa ana aamuna a mayi anga.+   Pakuti kudzipereka kwambiri panyumba yanu kwandidya,+ Ndipo mnyozo wa anthu amene akukutonzani wagwa pa ine.+ 10  Ndipo ndinalira ndi kusala kudya chifukwa cha moyo wanga,+ Koma anthu anali kungonditonza chifukwa cha zimenezo.+ 11  Pamene ndinavala ziguduli, Ndinakhala ngati mwambi kwa iwo.+ 12  Anthu okhala kuchipata anayamba kundidera nkhawa,+ Ndipo anthu amene anali kumwa zakumwa zoledzeretsa anali kundinena mu nyimbo zawo.+ 13  Koma ine ndinali kupemphera kwa inu Yehova,+ Pa nthawi yovomerezedwa, inu Mulungu.+ Ndiyankheni mwa kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha, ndipo sonyezani kuti ndinudi mpulumutsi.+ 14  Ndipulumutseni m’matope kuti ndisamire.+ Ndipulumutseni kwa anthu odana nane+ ndiponso ku madzi akuya.+ 15  Musalole kuti mtsinje wa madzi othamanga undikokolole,+ Kapena kuti madzi akuya andimize, Kapenanso kuti dzenje* lindimeze ndi kutseka pakamwa pake.+ 16  Ndiyankheni inu Yehova, pakuti kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwabwino.+ Ndicheukireni chifukwa chifundo chanu ndi chochuluka,+ 17  Ndipo ine mtumiki wanu musandibisire nkhope yanu.+ Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndasautsika kwambiri.+ 18  Yandikirani moyo wanga ndi kuupulumutsa.+ Ndiwomboleni kwa adani anga.+ 19  Inu mwadziwa chitonzo changa, manyazi anga ndi kunyazitsidwa kwanga.+ Onse odana nane ali pamaso panu.+ 20  Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+ Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+ Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+ 21  Koma anandipatsa chomera chakupha kuti ndidye,+ Ndipo anayesa kundimwetsa vinyo wowawasa pamene ndinali ndi ludzu.+ 22  Tebulo lawo likhale msampha,+ Ndipo akodwe ndi chilichonse chimene akusangalala nacho.+ 23  Maso awo achite mdima kuti asaone,+ Ndipo chititsani miyendo* yawo kunjenjemera mosalekeza.+ 24  Atsanulireni matemberero anu,+ Ndipo mkwiyo woyaka moto uwagwere.+ 25  Msasa wawo wokhala ndi mpanda ukhale bwinja,+ Ndipo m’mahema awo musapezeke munthu wokhalamo.+ 26  Pakuti iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,+ Ndipo amakamba za ululu wa anthu amene inu mwawalasa. 27  Wonjezerani zolakwa pa zolakwa zawo,+ Ndipo inu musawaone monga olungama.+ 28  Afafanizidwe m’buku la anthu amoyo,+ Ndipo iwo asalembedwe m’bukumo pamodzi ndi anthu olungama.+ 29  Koma ine ndasautsika ndipo ndikumva kupweteka.+ Inu Mulungu, chipulumutso chanu chinditeteze.+ 30  Ndidzatamanda dzina la Mulungu mwa kuimba nyimbo,+ Ndipo ndidzamulemekeza ndi nyimbo zomuyamika.+ 31  Zimenezinso zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ng’ombe yamphongo,+ Kuposa ng’ombe yamphongo yaing’ono imene ili ndi nyanga, komanso yogawanika ziboda.+ 32  Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.+ Inu amene mukutumikira Mulungu, mtima wanu ukhalenso ndi moyo.+ 33  Pakuti Yehova akumvetsera osauka,+ Ndipo sadzanyoza anthu ake amene ali m’ndende.+ 34  Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+ Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo.+ 35  Pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,+ Ndipo adzamanga mizinda ya Yuda,+ Iwo adzakhala mmenemo ndi kutenga dzikolo kukhala lawo.+ 36  Ana a atumiki ake adzalandira dzikolo monga cholowa chawo,+ Ndipo anthu okonda dzina lake adzakhala mmenemo.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Sl 45:Kamutu.
Zikuoneka kuti “dzenje” limeneli ndi manda.
Mawu ake enieni, “chiuno.”