Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 68:1-35

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ndi Salimo. 68  Mulungu anyamuke,+ adani ake amwazike,+ Ndipo amene amadana naye kwambiri athawe pamaso pake.+   Monga mmene mphepo imauluzira utsi, inunso muwauluze chimodzimodzi.+ Ngati mmene phula limasungunukira chifukwa cha moto,+ Anthu oipa awonongeke ndi kuchotsedwa pamaso pa Mulungu.+   Koma olungama asangalale,+ Asekerere pamaso pa Mulungu,+ Ndipo akondwere ndi kusangalala.+   Anthu inu, imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+ Muimbireni nyimbo Iye amene akudutsa m’chipululu,+ Amene dzina lake ndi Ya,*+ ndipo kondwerani pamaso pake.   Tate wa ana amasiye* ndi woweruzira akazi amasiye milandu,+ Ndi Mulungu amene amakhala m’malo ake oyera.+   Mulungu akuchititsa osungulumwa kukhala m’nyumba.+ Akumasula akaidi ndi kuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+ Koma anthu osamvera adzakhala m’dziko lowonongeka ndi kutentha kwa dzuwa.+   Inu Mulungu, pamene munatsogolera anthu anu,+ Pamene munadutsa  m’chipululu,+ [Seʹlah.]   Dziko lapansi linagwedezeka,+ Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,+ Phiri ili la Sinai linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu,+ Mulungu wa Isiraeli.+   Inu Mulungu, munayamba kugwetsa mvula yamphamvu,+ Ngakhale pamene anthu anu anali ofooka, inu munawalimbitsa.+ 10  Iwo anakhala mumsasa wanu wa mahema,+ Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino munakonzera munthu wosautsika msasa wa mahema.+ 11  Yehova wapereka lamulo,+ Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.+ 12  Mafumu enieniwo okhala ndi magulu a asilikali amathawa, ndithu amathawadi.+ Mkazi wongokhala pakhomo, nayenso amagwira nawo ntchito yofunkha.+ 13  Ngakhale anthu inu mutagona pakati pa milu ya phulusa mumsasawo, Mudzaona mapiko a njiwa okutidwa ndi siliva, Ndipo nthenga za kumapeto a mapiko ake zidzakhala zagolide wobiriwira monkera ku chikasu.+ 14  Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu a m’dzikomo,+ Mu Zalimoni+ munayamba kugwa chipale chofewa. 15  Dera lamapiri la ku Basana+ ndilo phiri la Mulungu.+ Dera lamapiri la ku Basana ndilo phiri la nsonga zitalizitali.+ 16  N’chifukwa chiyani inu mapiri a nsonga zitalizitali mumayang’ana mwanjiru Phiri limene Mulungu wafuna kukhalamo?+ Yehova adzakhala m’phiri limenelo mpaka muyaya.+ 17  Magaleta ankhondo a Mulungu ali m’magulu a masauzande makumimakumi, ali m’magulu a masauzande osawerengeka.+ Yehova walowa m’malo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+ 18  Mwakwera pamalo apamwamba,+ Mwatenga anthu ogwidwa,+ Mwatenga mphatso za amuna,+ Ndithu inu Yehova* Mulungu, mwatenga ngakhale anthu osamvera,+ kuti inu mukhale pakati pawo.+ 19  Adalitsike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+ Mulungu woona wa chipulumutso chathu.+ [Seʹlah.] 20  Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+ Ndipo njira zopulumukira ku imfa ndi za Yehova,+ Ambuye Wamkulu Koposa.+ 21  Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake kukhala zibenthuzibenthu,+ Adzaphwanya liwombo latsitsi la aliyense woyenda m’njira yochimwa.+ 22  Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+ Ndidzawatulutsa m’nyanja yakuya,+ 23  Kuti musambitse mapazi anu m’magazi,+ Kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.”+ 24  Iwo aona magulu anu a anthu opambana akuyendera pamodzi, inu Mulungu,+ Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akukalowa kumalo oyera.+ 25  Oimba nyimbo anali patsogolo, oimba zoimbira za zingwe anali pambuyo pawo,+ Pakati panali atsikana akuimba maseche.+ 26  Pamisonkhano tamandani Mulungu,+ Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+ 27  Pali fuko laling’ono la Benjamini limene likugonjetsa anthu,+ Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi makamu awo amene akufuula, Palinso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafitali.+ 28  Mulungu wanu walamula mphamvu zanu kuti zionekere.+ Inu Mulungu, sonyezani mphamvu monga mmene mwachitira kwa ife.+ 29  Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+ Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+ 30  Dzudzulani nyama yakutchire yokhala m’mabango,+ gulu la ng’ombe zamphongo,+ Pamodzi ndi mitundu ya anthu imene ili ngati ana a ng’ombe amphongo, aliyense amene akupondaponda ndalama zasiliva.+ Iye wabalalitsa mitundu ya anthu yokonda ndewu.+ 31  Zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina* zidzabwera kuchokera ku Iguputo,+ Mwamsanga Kusi adzatambasula dzanja lake ndi kupereka mphatso kwa Mulungu.+ 32  Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+ Imbani nyimbo zotamanda Yehova [Seʹlah.] 33  Imbirani Iye wokwera kumwamba kwa kumwamba kwakale.+ Tamverani! Iye akulankhula ndi mawu amphamvu.+ 34  Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+ Iye akulamulira Isiraeli ndipo mphamvu zake zili m’mitambo.+ 35  Mulungu akamatuluka m’malo ake opatulika aulemerero, amachititsa mantha.+ Iye ndi Mulungu wa Isiraeli, wopereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+ Mulungu adalitsike.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Mawu ake enieni, “ana aamuna opanda bambo.”
Mawu ake enieni, “Ya.” Onani mawu a m’munsi pa Eks 15:2.
Tanthauzo la mawu achiheberi amene tawamasulira kuti “zinthu zopangidwa ndi mkuwa wosakaniza ndi zitsulo zina” silidziwika. Ena amati tanthauzo lake ndi “akazembe.”