Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 67:1-7

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo. 67  Mulungu adzatiyanja ndi kutidalitsa.+ Iye adzatikomera mtima,+ [Seʹlah.]   Kuti njira zanu zidziwike padziko lapansi,+ Kuti chipulumutso chanu chidziwike pakati pa mitundu yonse ya anthu.+   Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+ Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+   Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+ Pakuti inu mudzaweruza anthu molungama.+ Ndipo mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. [Seʹlah.]   Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,+ Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.+   Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.+ Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.+   Mulungu adzatidalitsa,+ Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzamuopa.+

Mawu a M'munsi