Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 66:1-20

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo. 66  Inu anthu nonse padziko lapansi, fuulirani Mulungu mosangalala chifukwa wapambana.+   Imbani nyimbo zotamanda dzina lake.+M’patseni ulemerero ndi kumutamanda.   Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zanu, adani anu adzabwera kwa inu mogonjera.+   Anthu onse padziko lapansi adzakugwadirani,+Ndipo adzaimba nyimbo zokutamandani, adzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ [Seʹlah.]   Bwerani anthu inu, kuti muone ntchito za Mulungu.+Zimene wachitira ana a anthu ndi zochititsa mantha.+   Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,Anthu anawoloka mtsinje mwa kuyenda ndi mapazi awo.Pamenepo tinayamba kusangalala mwa iye.   Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+Maso ake akuyang’anitsitsa mitundu ya anthu.Koma anthu oumitsa khosi asadzikweze. [Seʹlah.]   Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,Chititsani mawu omutamanda kumveka.+   Iye amatisunga ndi moyo,Ndipo sanalole phazi lathu kupunthwa. 10  Pakuti inu Mulungu mwatisanthula,Mwatiyenga ngati siliva.+ 11  Mwatilowetsa mu ukonde wosakira nyama,+Mwatinyamulitsa katundu wolemera m’chiuno mwathu. 12  Mwachititsa munthu wamba kutipondaponda.+Tadutsa pamoto ndi pamadzi,+Ndipo inu mwatipatsa mpumulo.+ 13  Ndidzalowa m’nyumba yanu ndi nsembe zopsereza zathunthu.Ine ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu+ 14  Amene milomo yanga inanena,Ndiponso amene pakamwa panga pananena nthawi imene ndinali m’masautso aakulu. 15  Ndidzapereka kwa inu nsembe zathunthu zopsereza za nyama zonenepa,Pamodzi ndi nsembe zautsi wa nkhosa zamphongo.Ndidzapereka ng’ombe yamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo. [Seʹlah.] 16  Bwerani, mvetserani, inu nonse oopa Mulungu, ndipo ine ndifotokoza+Zimene wandichitira.+ 17  Ndinamuitana ndi pakamwa panga,+Ndipo ndinamutamanda ndi lilime langa.+ 18  Ngati ndikuganizira choipa chilichonse mumtima mwanga,Yehova sadzandimvera.+ 19  Ndithudi, Mulungu wamva,+Wamvetsera mwatcheru mawu a pemphero langa.+ 20  Adalitsike Mulungu amene sananyalanyaze pemphero langa,Kapena kundimana kukoma mtima kwake kosatha.

Mawu a M'munsi