Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Masalimo 65:1-13

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide. 65  Inu Mulungu, anthu akukutamandani mu Ziyoni+ ndipo akhala chete pamaso panu, Iwo adzakwaniritsa malonjezo awo kwa inu.+   Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+   Zolakwa zanga zandikulira.+ Inu mudzatikhululukira* machimo athu.+   Wodala ndi munthu amene inu mwamusankha ndi kumuyandikizitsa kwa inu,+ Kuti akhale m’mabwalo anu.+ Tidzakhutira ndi zinthu zabwino za m’nyumba yanu,+ Malo anu oyera kapena kuti kachisi wanu woyera.+   Mudzatiyankha ndi zinthu zochititsa mantha zochitika mwachilungamo,+ Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,+ Inu Chidaliro cha malire onse a dziko lapansi ndi anthu okhala pafupi ndi nyanja zakutali.+   Ndi mphamvu zake, iye akukhazikitsa mapiri,+ Iye wamanga mphamvu zochuluka m’chiuno mwake.+   Iye akutontholetsa phokoso la nyanja,+ Akutontholetsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+   Ndipo anthu okhala m’madera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu,+ Mudzachititsa kulowa ndi kutuluka kwa dzuwa kufuula mokondwera.+   Inu mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka,+ Mwalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wosefukira ndi madzi.+ Munalinganiza zinthu, kuti mbewu zawo zibale.+ Umu ndi mmene mumaperekera zinthu padziko lapansi.+ 10  Mizere yawo imakhathamira, ndipo zibuma zake zimasalazidwa,+ Ndipo mumafewetsa nthaka ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera m’nthakayo.+ 11  Mwaveka chaka chisoti chachifumu cha ubwino wanu,+ Ndipo njira zanu zikukha mafuta.+ 12  Malo odyetserako ziweto a m’chipululu akukha mafuta,+ Ndipo zitunda zamangirira chisangalalo m’chiuno mwawo.+ 13  Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,+ Ndipo zigwa zakutidwa ndi tirigu.+ Malo onsewa akufuula mosangalala ndi kuimba chifukwa cha kupambana.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mudzaphimba.”