Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 64:1-10

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide. 64  Inu Mulungu, imvani mawu ofotokoza nkhawa zanga.+ Tetezani moyo wanga kuti usaope mdani.+   Ndibiseni kuti ndisamve zinsinsi za anthu ochita zoipa,+ Kuti ndisamve phokoso la anthu ochita zovulaza anzawo,+   Amene anola lilime lawo ngati lupanga,+ Amene alunjikitsa mivi yawo, imene ndi mawu awo owawa,+   Pa munthu wosalakwa, kuti amulase atamubisalira.+ Amamulasa modzidzimutsa ndipo saopa.+   Amaumirira kulankhula zoipa,+ Amakambirana kuti atchere misampha.+ Iwo amati: “Angaione ndani?”+   Amafunafuna kuchita zinthu zosalungama,+ Abisa chiwembu chimene achikonza mochenjera,+ Ndipo zamkati, zamumtima mwa aliyense, n’zovuta kuzimvetsa.+   Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi modzidzimutsa.+ Iwo adzakhala ndi zilonda,+   Ndipo iwo amakhumudwitsa munthu,+ Koma lilime lawo likutsutsana nawo.+ Onse owayang’ana adzapukusa mitu yawo,+   Anthu onse adzachita mantha,+ Ndipo adzanena za ntchito za Mulungu,+ Iwo adzamvetsa bwino ntchito zake.+ 10  Wolungama adzakondwera mwa Yehova ndipo adzathawira kwa iye,+ Ndipo onse owongoka mtima adzatamanda Mulungu.+

Mawu a M'munsi