Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 63:1-11

Nyimbo ya Davide pamene anali m’chipululu cha Yuda.+ 63  Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+ Moyo wanga ukulakalaka inu.+ Thupi langa lalefuka chifukwa cholakalaka inu M’dziko louma ndi lopanda chonde, lopanda madzi.+   Choncho ndakuonani m’malo oyera,+ Chifukwa ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+   Pakuti kukoma mtima kwanu kosatha n’kwabwino kuposa moyo,+ Milomo yanga idzakuyamikirani.+   Choncho ndidzakutamandani pa nthawi yonse ya moyo wanga.+ Ndidzapemphera m’dzina lanu nditakweza manja anga.+   Moyo wanga wakhutira ndi gawo labwino kwambiri, wakhutira ndi zinthu zabwino kwambiri,+ Ndipo milomo yanga ikukutamandani ndi mfuu yachisangalalo.+   Ndikakumbukira inu ndili pabedi langa,+ Pa nthawi za ulonda wa usiku* ndimasinkhasinkha za inu.+   Pakuti mwandithandiza,+ Ndipo mumthunzi wa mapiko anu ndimafuula mosangalala.+   Ndakulondolani kulikonse,+ Dzanja lanu lamanja landigwira mwamphamvu.+   Koma ofuna kuwononga moyo wanga,+ Adzatsikira kumanda.+ 10  Adzaphedwa ndi lupanga,+ Adzakhala chakudya cha nkhandwe.+ 11  Ndipo mfumu idzakondwera mwa Mulungu.+ Aliyense wolumbira m’dzina la Mulungu adzam’tamanda,+ Pakuti pakamwa pa anthu olankhula chinyengo padzatsekedwa.+

Mawu a M'munsi

Pa nthawi ya Mfumu Davide, Aisiraeli anali ndi maulonda a usiku atatu. Ulonda woyamba unkayamba 6 koloko madzulo mpaka 10 koloko usiku. Ulonda wachiwiri unkayamba 10 koloko usiku mpaka 2 koloko usiku, ndipo ulonda wachitatu unkayamba 2 koloko usiku mpaka 6 koloko m’mawa.